Yeremiya 20:16 - Buku Lopatulika16 Munthuyo akhale ngati mizinda imene Yehova anapasula, osalekerera; amve mfuu mamawa, ndi mkuwo pausana; Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201416 Munthuyo akhale ngati midzi imene Yehova anapasula, osalekerera; amve mfuu mamawa, ndi mkuwo pausana; Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa16 Munthu ameneyo akhale ngati mizinda imene adaiwononga Chauta mopanda chifundo ija. Amve kulira kwa kupweteka m'maŵa, ndiponso phokoso la nkhondo masana, Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero16 Munthu ameneyo akhale ngati mizinda imene Yehova anayiwononga mopanda chisoni. Amve mfuwu mmawa, phokoso la nkhondo masana. Onani mutuwo |
Chifukwa chake, pali moyo wanga, ati Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, Zedi Mowabu adzakhala ngati Sodomu, ndi ana a Amoni ngati Gomora, pochuluka khwisa ndi maenje a mchere, ndi bwinja losatha; otsala a anthu anga adzalanda zao, ndi otsala a mtundu wa anthu anga adzawalandira akhale cholowa chao.