Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 2:28 - Buku Lopatulika

28 Koma ili kuti milungu yako imene wadzipangira? Iuke, ikupulumutse iwe m'nthawi ya kuvutidwa kwako; pakuti milungu yako ilingana ndi kuchuluka kwa mizinda yako, Yuda iwe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

28 Koma ili kuti milungu yako imene wadzipangira? Iuke, ikupulumutse iwe m'nthawi ya kuvutidwa kwako; pakuti milungu yako ilingana ndi kuchuluka kwa midzi yako, Yuda iwe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

28 Nanga milungu yanu ili kuti, milungu ija mudadzipangira ija? Idzambatuketu, ngati ingathe kukupulumutsani pa nthaŵi yanu ya mavuto. Inu anthu a ku Yuda, milungu yanu ndi yambiri, kuchuluka kwake monga momwe iliri mizinda yanu.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

28 Nanga ili kuti milungu yanu imene munadzipangira nokha? Ibweretu ngati ingathe kukupulumutsani pamene muli pamavuto! Inu anthu a ku Yuda, milungu yanu ndi yambiri kuchuluka kwake ngati mizinda yanu.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 2:28
16 Mawu Ofanana  

Ndipo Elisa anati kwa mfumu ya Israele, Ndili ndi chiyani ndi inu? Mukani kwa aneneri a atate wanu, ndi kwa aneneri a amai wanu. Koma mfumu ya Israele inanena naye, Iai, pakuti Yehova anaitana mafumu ife atatu kutipereka m'dzanja la Mowabu.


Sonkhanani nokha, mudze; yandikirani chifupi pamodzi, inu amene mwapulumuka amitundu; iwo alibe nzeru, amene anyamula mtengo wa fano lao losema, ndi kupemphera mulungu wosakhoza kupulumutsa.


Milunguyo iwerama, igwada pansi pamodzi; singapulumutse katundu, koma iyo yeni yalowa m'ndende.


Iwo amanyamula mlunguwu paphewa, nausenza, naukhazika m'malo mwake, nukhala chilili; pamalo pakepo sudzasunthika; inde, wina adzaufuulira, koma sungathe kuyankha, kapena kumpulumutsa m'zovuta zake.


Pamene pakufuula iwe akupulumutse amene unawasonkhanitsa; koma mphepo idzawatenga, mpweya udzachotsa onse; koma iye amene andikhulupirira Ine adzakhala ndi dziko, nadzakhala nacho cholowa m'phiri langa lopatulika.


Ndipo ndidzanena nao za maweruzo anga akuweruzira zoipa zao zonse; popeza anandisiya Ine, nafukizira milungu ina, nagwadira ntchito za manja ao.


Ndipo mizinda ya Yuda ndi okhala mu Yerusalemu adzapita nadzafuulira kwa milungu imene anaifukizira; koma siidzawapulumutsa konse nthawi ya nsautso yao.


Pakuti milungu yako ilingana ndi kuchuluka kwa mizinda yako, iwe Yuda; ndi maguwa a nsembe amene mwautsira chamanyazi, alingana ndi kuchuluka kwa miseu ya Yerusalemu, ndiwo maguwa akufukizirapo Baala.


Kalanga ine! Pakuti nlalikulu tsikulo, palibe lina lotere; ndi nthawi ya msauko wa Yakobo; koma adzapulumuka m'menemo.


Tsopano ali kuti aneneri anu, amene ananenera inu, kuti, Mfumu ya ku Babiloni sidzakudzerani inu, kapena dziko lino?


Israele ndi mpesa wotambalala, wodzibalira wokha zipatso; monga umo zinachulukira zipatso zake, momwemo anachulukitsa maguwa a nsembe ake; monga mwa kukoma kwake kwa dziko lake anapanga zoimiritsa zokoma.


Apindulanji nalo fano losema, kuti wakulipanga analisema; fano loyenga ndi mphunzitsi wamabodza, kuti wakulipanga alikhulupirira, atapanga mafano osanena mau?


Tsoka iye wakunena kwa mtengo, Galamuka; ndi kwa mwala wosalankhula, Nyamuka! Kodi ichi chiphunzitsa? Taona chakutidwa ndi golide ndi siliva, ndi m'kati mwake mulibe mpweya konse.


Pamenepo adzati, Ili kuti milungu yao, thanthwe limene anathawirako?


Mukani ndi kufuulira kwa milungu munaisankha, ikupulumutseni nyengo ya kusauka kwanu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa