Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 2:27 - Buku Lopatulika

27 amene ati kwa mtengo, Iwe ndiwe atate wanga; ndi kwa mwala, Wandibala; pakuti anandipatsa Ine mbuyo, si nkhope yao; koma m'nthawi ya kuvutidwa kwao adzati, Ukani, tipulumutseni.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

27 amene ati kwa mtengo, Iwe ndiwe atate wanga; ndi kwa mwala, Wandibala; pakuti anandipatsa Ine mbuyo, si nkhope yao; koma m'nthawi ya kuvutidwa kwao adzati, Ukani, tipulumutseni.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

27 Amauza mtengo kuti ‘Iwe ndiwe bambo wathu,’ amauza mwala kuti ‘Iwe ndiwe amene udatibala.’ Koma Ine amandifulatira, m'malo motembenukira kwa Ine. Tsono akakhala pa mavuto amati, ‘Dzambatukani, mutithandize.’

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

27 Iwo amawuza mtengo kuti, ‘Iwe ndiwe abambo athu,’ ndipo amawuza mwala kuti, ‘Iwe ndiye amene unatibala.’ Iwo andifulatira Ine, ndipo safuna kundiyangʼana; Koma akakhala pa mavuto amati, ‘Bwerani mudzatipulumutse!’

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 2:27
23 Mawu Ofanana  

Pakuti analakwa makolo athu, nachita choipa pamaso pa Yehova Mulungu wathu, namsiya, natembenuza nkhope zao osapenya chokhalamo Yehova, namfulatira.


Yehova, iwo adza kwa Inu movutika, iwo anathira pemphero, muja munalikuwalanga.


Koma onse pamodzi apulukira ndi kupusa; mtengo ndiwo chilangizo, chopanda pake.


Ndidzamwazamwaza iwo monga ndi mphepo ya kum'mawa pamaso pa adani; ndidzayang'anira pamsana pao, si nkhope yao, tsiku la Tsoka lao.


mbidzi yozolowera m'chipululu, yopumira mphepo pakufuna pake; pokomana nayo ndani adzaibweza? Onse amene aifuna sadzadzilemetsa; adzaipeza m'mwezi wake.


Iwe wokhala mu Lebanoni, womanga chisa chako m'mikungudza, udzachitidwa chisoni chachikulu nanga pamene mapweteko adzadza kwa iwe, monga mkazi alinkudwala!


Ndipo kunali kuti mbiri ya dama lake inaipitsa dziko, ndipo anachita chigololo ndi miyala ndi mitengo.


Kalanga ine! Pakuti nlalikulu tsikulo, palibe lina lotere; ndi nthawi ya msauko wa Yakobo; koma adzapulumuka m'menemo.


Ndipo anandipatsa Ine mbuyo, si nkhope, ngakhale ndinawaphunzitsa, kuuka m'mamawa ndi kuwaphunzitsa, koma sanamvere kulangizidwa.


Ndipo Zedekiya mfumu anatuma Yehukala mwana wa Selemiya, ndi Zefaniya mwana wa Maaseiya wansembe, kwa Yeremiya mneneri, kukanena, Mutipemphereretu kwa Yehova Mulungu wathu.


nati kwa Yeremiya mneneri, Chipembedzero chathu chigwe pamaso panu, nimutipempherere ife kwa Yehova Mulungu wanu, chifukwa cha otsala onsewa; pakuti tatsala ife owerengeka m'malo mwa ambiri, monga maso anu ationa ife;


Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Popeza wandiiwala Ine, ndi kunditaya pambuyo pako, uzisenza iwenso choipa chako ndi zigololo zako.


Ndipo anadza nane ku bwalo lam'kati la nyumba ya Yehova, ndipo taonani, pa khomo la Kachisi wa Yehova, pakati pa khonde lake ndi guwa la nsembe, panali amuna ngati makumi awiri mphambu asanu akufulatira, ku Kachisi wa Yehova, ndi kuyang'ana kum'mawa, napembedza dzuwa kum'mawa.


Ambuye, chilungamo ncha Inu, koma kwa ife manyazi a nkhope yathu, monga lero lino; kwa anthu a Yuda, ndi kwa okhala mu Yerusalemu, ndi kwa Aisraele onse okhala pafupi ndi okhala kutali, kumaiko onse kumene mudawaingira, chifukwa cha kulakwa kwao anakulakwirani nako.


Anthu anga afunsira kumtengo wao, ndi ndodo yao iwafotokozera; pakuti mzimu wachigololo wawalakwitsa, ndipo achita chigololo kuchokera Mulungu wao.


Ndidzamuka ndi kubwerera kunka kumalo kwanga, mpaka adzavomereza kupalamula kwao, nafunafuna nkhope yanga; m'msauko mwao adzandifunafuna mwachangu.


Ndipo sanafuulire kwa Ine ndi mtima wao, koma alira pakama pao, asonkhanira tirigu ndi vinyo, apikisana ndi Ine.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa