Yeremiya 2:25 - Buku Lopatulika25 Kaniza phazi lako lisakhale losavala nsapato, ndi m'mero mwako musakhale ndi ludzu; koma unati, Palibe chiyembekezo, iai; pakuti ndakonda alendo, ndipo ndidzatsata pambuyo pao. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201425 Kaniza phazi lako lisakhale losavala nsapato, ndi m'mero mwako musakhale ndi ludzu; koma unati, Palibe chiyembekezo, iai; pakuti ndakonda alendo, ndipo ndidzatsata pambuyo pao. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa25 Iwe Israele, lekatu, nsapato zingakuthere ku phazi, kukhosi kwako kungaume ndi ludzu potsatira milungu ina. Koma iwe ukuti, ‘Ai toto, sindingathe kuchitira mwina, ndimakonda milungu yachilendoyi, sindingaleke kuitsata.’ Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero25 Iwe usathamange, nsapato zingakuthere kuphazi ndi kukhosi kwako kuwuma ndi ludzu. Koma unati, ‘Zamkutu! Ine ndimakonda milungu yachilendo, ndipo ndidzayitsatira.’ Onani mutuwo |
Koma tidzachita ndithu mau onse anatuluka m'kamwa mwathu, kufukizira mfumu yaikazi ya kumwamba, ndi kumthirira iye nsembe zothira, monga momwe tinkachitira ife, ndi atate athu, ndi mafumu athu ndi akulu athu, m'mizinda ya Yuda, ndi m'miseu ya Yerusalemu, pakuti pamenepo tinali ndi chakudya chokwanira, tinakhala bwino, sitinaona choipa.