Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 2:22 - Buku Lopatulika

22 Pakuti ngakhale usamba ndi soda, ndi kudzitengera sopo wambiri, mphulupulu zako zidziwika pamaso panga, ati Yehova Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 Pakuti ngakhale usamba ndi soda, ndi kudzitengera sopo wambiri, mphulupulu zako zidziwika pamaso panga, ati Yehova Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 Ngakhale usambire soda, ngakhale usambire sopo wambiri, kuthimbirira kwa tchimo lako kumaonekabe pamaso panga,” akuterotu Ambuye Chauta.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 Ngakhale utasamba ndi soda kapena kusambira sopo wambiri, kuthimbirira kwa machimo ako kumaonekabe pamaso panga,” akutero Ambuye Yehova.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 2:22
12 Mawu Ofanana  

Ndipo Davide anati kwa Uriya, Utsotse pano leronso, ndipo mawa ndidzakulola umuke. Chomwecho Uriya anakhala ku Yerusalemu tsiku lomwelo ndi m'mawa mwake.


Cholakwa changa chaikidwa m'thumba lokhomedwa chizindikiro; ndipo mumanga pamodzi mphulupulu zanga.


Mukasunga mphulupulu, Yehova, adzakhala chilili ndani, Ambuye?


Munaika mphulupulu zathu pamaso panu, ndi zoipa zathu zobisika pounikira nkhope yanu.


Pakuti maso anga ali panjira zao zonse, sabisika pa nkhope yanga, mphulupulu yao siibisika pamaso panga.


Tchimo la Yuda lalembedwa ndi peni lachitsulo, ndi nsonga ya diamondi; lalembedwa pa cholembapo cha m'mtima mwao, ndi pa nyanga za maguwa a nsembe ao.


Iwe Yerusalemu, utsuke mtima wako kuchotsa zoipa kuti upulumuke. Maganizo ako achabe agona mwako masiku angati?


Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Tsoka mzinda wokhetsa mwazi, mphika m'mene muli dzimbiri, losauchokera dzimbiri lake; uchotsemo chiwalochiwalo; sanaugwere maere.


Mphulupulu ya Efuremu yamangika, tchimo lake lisungika.


Yehova walumbira pali kudzikuza kwa Yakobo, Ngati ndidzaiwala konse ntchito zao zilizonse?


Kodi sichisungika ndi Ine, cholembedwa chizindikiro mwa chuma changa chenicheni?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa