Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 2:14 - Buku Lopatulika

14 Kodi Israele ndi mtumiki? Kodi ndiye kapolo wobadwa m'nyumba? Afunkhidwa bwanji?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Kodi Israele ndi mtumiki? Kodi ndiye kapolo wobadwa m'nyumba? Afunkhidwa bwanji?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 “Israele si kapolotu ai, sadabadwire mu ukapolo. Nanga chifukwa chiyani amuwononga chotere?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Israeli si wantchito kapena kapolo wobadwira mʼnyumba, ayi. Nanga nʼchifukwa chiyani amuwononga chotere?

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 2:14
7 Mawu Ofanana  

Ndipo Abramu anati, Taonani, simunandipatse ine mbeu; ndipo, taonani, wobadwa m'nyumba mwanga adzalowa m'malo mwanga.


Pakhale lamulo lomweli pa wobadwa m'dziko, ndi pa mlendo wakukhala pakati pa inu.


Pamenepo ukanene ndi Farao, Atero Yehova Mwana wanga, mwana wanga woyamba ndiye Israele.


ndinadzitengera akapolo ndi adzakazi, ndinali ndi akapolo anabadwa kwanga; ndinalemeranso pokhala nazo zoweta zazikulu ndi zazing'ono kupambana onse anakhala mu Yerusalemu ndisanabadwe ine;


Atero Yehova, Kalata ya chilekaniro cha amai ako ali kuti amene ndinamsudzula naye? Pena ndani wa angongole anga amene ndamgulitsa iwe? Taona chifukwa cha zoipa zanu munagulitsidwa, ndi chifukwa cha kulakwa kwanu amanu anachotsedwa.


Iwe, iwe wekha, udzaleka pa cholowa chako chimene ndinakupatsa iwe; ndipo ndidzakutumikiritsa adani ako m'dziko limene sulidziwa; pakuti wakoleza moto m'mkwiyo wanga umene udzatentha kunthawi zamuyaya.


Ndipo padzakhala pamene mudzati, Chifukwa chanji Yehova Mulungu wathu atichitira ife zonse izi? Ndipo udzayankha kwa iwo, Monga ngati mwandisiya Ine, ndi kutumikira milungu yachilendo m'dziko lanu, momwemo mudzatumikira alendo m'dziko silili lanu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa