Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 19:9 - Buku Lopatulika

9 Ndipo ndidzadyetsa iwo mnofu wa ana ao aamuna ndi aakazi, ndipo adzadya yense mnofu wa mbale wake, m'nkhondo yozinga ndi m'kupsinjikako, kumene adani ao, ndi iwo akufuna moyo wao, adzapsinja iwo nako.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Ndipo ndidzadyetsa iwo mnofu wa ana ao aamuna ndi aakazi, ndipo adzadya yense mnofu wa mbale wake, m'nkhondo yozinga ndi m'kupsinjikako, kumene adani ao, ndi iwo akufuna moyo wao, adzapsinja iwo nako.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Ndidzaumiriza anthuwo kuti adye ana ao omwe aamuna ndi aakazi. Adzadyana choncho pa nthaŵi yoopsa pamene adzazingidwa ndi adani ao ofuna kuŵazunza.’

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Adani awo adzawuzinga mzindawo kufuna kuwapha motero kuti anthu a mʼkatimo adzafika pomadyana wina ndi mnzake. Adzadya ana awo aamuna ndi ana awo aakazi.’

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 19:9
10 Mawu Ofanana  

Tsiku lachisanu ndi chinai la mwezi wachinai njala idakula m'mzindamo, panalibe chakudya kwa anthu a m'dzikomo.


Ndipo wina adzakwatula ndi dzanja lamanja, nakhala ndi njala; ndipo adzadya ndi dzanja lamanzere, osakhutai; iwo adzadya munthu yense nyama ya mkono wake wa iye mwini.


Ndipo ndidzaphwanyanitsa wina ndi wina, atate ndi ana, ati Yehova; sindidzakhala ndi chisoni, sindidzapulumutsa, sindidzakhala ndi chifundo, chakuti ndisawaononge.


Mbuyanga mfumu, anthu awa anachita zoipa m'zonse anachitira Yeremiya mneneri, amene anamponya m'dzenje; ndipo afuna kufa m'menemo chifukwa cha njala; pakuti mulibe chakudya china m'mzindamu.


Onani Yehova, nimupenye, mwachitira ayani ichi? Kodi akazi adzadya zipatso zao, kunena ana amene anawalera wokha? Kodi wansembe ndi mneneri adzaphedwa m'malo opatulika a Ambuye?


Manja a akazi achisoni anaphika ana aoao; anali chakudya chao poonongeka mwana wamkazi wa anthu a mtundu wanga.


Chifukwa chake atate adzadya ana pakati pako, ndi ana adzadya atate ao; ndipo ndidzachita maweruzo mwa iwe, ndi akutsala onse ndidzawabalalitsa kumphepo zonse.


Ndipo mudzadya nyama ya ana anu aamuna; inde nyama ya ana anu aakazi mudzaidya.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa