Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 19:8 - Buku Lopatulika

8 Ndipo ndidzayesa mzindawu chodabwitsa, ndi chotsonyetsa; onse amene adzapitapo adzadabwa ndi kutsonya chifukwa cha zopanda pake zonse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Ndipo ndidzayesa mudziwu chodabwitsa, ndi chotsonyetsa; onse amene adzapitapo adzadabwa ndi kutsonya chifukwa cha zopanda pake zonse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Mzinda umenewu ndidzausandutsa malo ochititsa nyansi ndiponso odzetsa mfuu wa mantha. Aliyense wodutsapo adzachita nawodi nyansi ndipo adzafuula ndi mantha poona kukanthidwa kwake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Mzinda uno ndidzawusakaza ndi kuwusandutsa chinthu chochititsa mantha ndi chonyansa. Onse odutsamo adzadabwa ndi kupukusa mitu yawo chifukwa cha kuwonongeka kwake.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 19:8
14 Mawu Ofanana  

Ndipo munthu yense wopitirira pa nyumba yaitali ino adzadabwa nayo, nadzainyoza, nadzati, Yehova watero chifukwa ninji ndi dziko lino ndi nyumba ino?


kuti aliyense dziko lao likhale lodabwitsa, ndi kutsonya chitsonyere; yense wakupitapo adzadabwa, ndi kupukusa mutu wake.


Yerusalemu, ndi mizinda ya Yuda, ndi mafumu ake omwe, ndi akulu ake, kuwayesa iwo bwinja, chizizwitso, chotsonyetsa, ndi chitemberero; monga lero lino;


Pakuti ndalumbira, Pali Ine ati Yehova, kuti Bozira adzakhala chizizwitso, chitonzo, chopasuka, ndi chitemberero; ndipo mizinda yake yonse idzakhala yopasuka chipasukire.


Chifukwa cha mkwiyo wa Yehova sadzakhalamo anthu, koma padzakhala bwinja; onse akupita pa Babiloni adzadabwa, adzatsonyera pa zovuta zake zonse.


Amalonda mwa mitundu ya anthu akunyodola, wakhala choopsetsa iwe, ndipo sudzakhalanso konse.


Inde, ndidzapasula dzikoli, ndipo adani anu akukhala m'mwemo adzadabwa nako.


Pakuti asunga malemba a Omuri, ndi ntchito za nyumba ya Ahabu, ndipo mumayenda mu uphungu wao; kuti ndikusandulize bwinja, ndi okhalamo chotsonya; ndipo mudzasenza chitonzo cha anthu anga.


Uwu ndi mzinda wosekererawo unakhala wosasamalira, unanena m'mtima mwake, Ine ndine, ndi wopanda ine palibe wina; ha! Wasanduka bwinja, mogonera nyama zakuthengo! Yense wakuupitirira adzatsonya mtsonyo, ndi kupukusa mutu.


Ndipo mudzakhala chodabwitsa, ndi nkhani, ndi mwambi, mwa mitundu yonse ya anthu amene Yehova akutsogoleraniko.


Ndipo mbadwo ukudza, ana anu akuuka mutafa inu, ndi mlendo wochokera ku dziko lakutali, adzati, pakuona iwo miliri ya dziko ili, ndi nthendazi, Yehova awadwalitsa nazo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa