Yeremiya 19:11 - Buku Lopatulika11 nuziti kwa iwo, Yehova wa makamu atero: Chomwecho ndidzaphwanya anthu awa ndi mzinda uwu, monga aphwanya mbiya ya woumba, imene sangathe kuiumbanso, ndipo adzaika maliro mu Tofeti, mpaka mulibe malo akuikamo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201411 nuziti kwa iwo, Yehova wa makamu atero: Chomwecho ndidzaphwanya anthu awa ndi mudzi uwu, monga aphwanya mbiya ya woumba, imene sangathe kuiumbanso, ndipo adzaika maliro m'Tofeti, mpaka mulibe malo akuikamo. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa11 Ndiye udzaŵauze kuti, Chauta Wamphamvuzonse akuti, Umu ndi m'mene ndidzaonongere anthu ameneŵa, monga momwe woumba amaphwanyira mbiya yake, kotero kuti sangathenso kuikonza. Anthu akufawo adzaŵaika ku Tofeti, chifukwa choti kwina kulikonse sikudzakhala malo oŵaika. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero11 ndipo ukawawuze kuti, ‘Yehova Wamphamvuzonse akuti, Ine ndidzaphwanya dziko lino ndi mzinda uno ngati momwe wowumba amaphwanyira mbiya yake ndipo sangathe kuyikonzanso. Adzayika anthu akufa ku Tofeti chifukwa padzasowa malo ena owayika. Onani mutuwo |