Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 19:1 - Buku Lopatulika

1 Atero Yehova, Pita, nugule nsupa ya woumba, nutenge akulu a anthu, ndi akulu a ansembe;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Atero Yehova, Pita, nugule nsupa ya woumba, nutenge akulu a anthu, ndi akulu a ansembe;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Chauta adandiwuza kuti, “Pita ukagule mtsuko wadothi kwa munthu woumba. Utenge akuluakulu ena, ndiponso ansembe ena okhwimapo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Yehova anandiwuza kuti, “Pita ukagule mʼphika wadothi kwa munthu wowumba. Utenge akuluakulu ena a anthuwa ndi ansembe

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 19:1
20 Mawu Ofanana  

Natuma Eliyakimu woyang'anira nyumbayo, ndi Sebina mlembi, ndi akulu a ansembe ofundira chiguduli, kwa Yesaya mneneri mwana wa Amozi.


Ndipo Iye adzagumulapo, monga mbiya ya woumba isweka, ndi kuiswaiswa osaileka; ndipo sipadzapezedwa m'zigamphu zake phale lopalira moto pachoso, ngakhale lotungira madzi padziwe.


Atero Yehova kwa ine, Pita, udzigulire mpango wabafuta, nudzimangire m'chuuno mwako, usauike m'madzi.


Ndipo anauka akulu ena a m'dziko, nati kwa msonkhano wa anthu, kuti,


Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele atero; Tenga makalata awa, kalata yogulira, yosindikizidwa, ndi kalata yovundukuka, nuwaike m'mbiya yadothi; kuti akhale masiku ambiri.


Ana a Ziyoni a mtengo wapatali, olingana ndi golide woyengetsa, angoyesedwa ngati mbiya zadothi zozipanga manja a woumba.


Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, dzitengere njerwa, nuiike pamaso pako, nulembepo mzinda, ndiwo Yerusalemu;


Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, udzitengere mpeni wakuthwa, ndiwo lumo la wometa, udzitengere ndi kulipititsa pamutu pako ndi pa ndevu zako; nudzitengere muyeso kuyesa nao, ndi kugawa tsitsilo.


iphanitu nkhalamba, mnyamata ndi namwali, makanda, ndi akazi; koma musayandikira munthu aliyense ali nacho chizindikiro, ndipo muyambe pamalo anga opatulika. Pamenepo anayamba ndi akuluwo anali pakhomo pa nyumba.


Ndipo Yehova anati kwa Mose, Undisonkhanitsire amuna makumi asanu ndi awiri mwa akulu a Israele, amene uwadziwa kuti ndiwo akulu a anthu, ndi akapitao ao; nubwere nao ku chihema chokomanako, kuti aimeko pamodzi ndi iwe.


Pomwepo anasonkhana ansembe aakulu, ndi akulu a anthu, kubwalo la mkulu wa ansembe, dzina lake Kayafa;


Ndipo pakudza mamawa, ansembe aakulu ndi akulu a anthu onse anakhala upo wakumchitira Yesu, kuti amuphe;


Ndipo anadza kwa ife natenga lamba la Paulo, nadzimanga yekha manja ndi mapazi, nati, Atero Mzimu Woyera, Munthu mwini lamba ili, adzammanga kotero Ayuda a mu Yerusalemu, nadzampereka m'manja a amitundu.


Koma tili nacho chuma ichi m'zotengera zadothi, kuti ukulu woposa wamphamvu ukhale wa Mulungu, wosachokera kwa ife;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa