Yeremiya 18:6 - Buku Lopatulika6 Nyumba ya Israele inu, kodi sindingathe kuchita ndi inu monga woumba uyu? Ati Yehova. Taonani, monga dothi m'dzanja la woumba, momwemo inu m'dzanja langa, nyumba ya Israele. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20146 Nyumba ya Israele inu, kodi sindingathe kuchita ndi inu monga woumba uyu? Ati Yehova. Taonani, monga dothi m'dzanja la woumba, momwemo inu m'dzanja langa, nyumba ya Israele. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa6 “Inu Aisraele, kodi Ine sindingathe kuchita nanu monga amachitira woumba mbiya? Zedi, inuyo muli m'manja mwangamu monga momwe umakhalira mtapo m'manja mwa woumba mbiya. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero6 “Inu Aisraeli, kodi Ine sindingathe kuchita nanu monga amachitira wowumba mbiya?” akutero Yehova. “Inu muli mʼmanja mwanga ngati mtapo mʼmanja mwa wowumba mbiya. Onani mutuwo |
Tsono, kuti mfumu inaona mthenga woyera wotsika kumwamba, ndi kuti, Likhani mtengowo ndi kuuononga, koma siyani chitsa chake ndi mizu m'nthaka, chomangidwa ndi mkombero wa chitsulo ndi mkuwa, mu msipu wakuthengo, ndipo chikhale chokhathamira ndi mame a kumwamba, ndi gawo lake likhale pamodzi ndi nyama zakuthengo, mpaka zitampitira nthawi zisanu ndi ziwiri;