Yeremiya 18:16 - Buku Lopatulika16 kuti aliyense dziko lao likhale lodabwitsa, ndi kutsonya chitsonyere; yense wakupitapo adzadabwa, ndi kupukusa mutu wake. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201416 kuti aliyense dziko lao likhale lodabwitsa, ndi kutsonya chitsonyere; yense wakupitapo adzadabwa, ndi kupukusa mutu wake. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa16 Dziko lao amalisandutsa lochititsa nyansi ndi lodzetsa mfuu wa mantha mpaka muyaya. Aliyense wodutsamo adzakhala akudabwa ndi kumapukusa mutu. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero16 Dziko lawo amalisandutsa chipululu, chinthu chochititsa manyazi nthawi zonse; onse odutsapo adzadabwa kwambiri ndipo adzapukusa mitu yawo. Onani mutuwo |
taonani, Ine, ndidzatuma ndi kutenga mabanja onse a kumpoto, ati Yehova, ndipo ndidzatuma kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, mtumiki wanga, ndipo ndidzatengera iwo padziko lino, ndi pa okhalamo ake onse, ndi pa mitundu iyi yozungulira, ndipo ndidzathetsa iwo ndithu, ndi kuwayesa iwo chizizwitso, ndi chotsonyetsa, ndi bwinja lamuyaya.
Pakuti atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Monga mkwiyo wanga ndi ukali wanga wathiridwa kwa okhala mu Yerusalemu, momwemo ukali wanga udzathiridwa pa inu, pamene mudzalowa mu Ejipito; ndipo mudzakhala chitukwano, ndi chizizwitso, ndi chitemberero, ndi chitonzo; ndipo simudzaonananso malo ano.
Ndipo ndidzatenga otsala a Yuda, amene analozetsa nkhope zao alowe m'dziko la Ejipito akhale m'menemo, ndipo adzathedwa onse; m'dziko la Ejipito adzagwa, adzathedwa ndi lupanga ndi njala; adzafa kuyambira wamng'ono mpaka wamkulu, ndi lupanga ndi njala; ndipo adzakhala chitukwano, ndi chizizwitso, ndi chitemberero, ndi chitonzo.