Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 18:13 - Buku Lopatulika

13 Chifukwa chake atero Yehova; Funsanitu m'mitundu, ndani wamva zotero; namwali wa Israele wachita chinthu choopsetsa kwambiri.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Chifukwa chake atero Yehova; Funsanitu m'mitundu, ndani wamva zotero; namwali wa Israele wachita chinthu choopsetsa kwambiri.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Nchifukwa chake Chauta akunena kuti, “Ukafunse anthu a mitundu ina yonse, ngati alipo amene adamvapo zotere. Israele amene adaali ngati namwali wosadziŵa mwamuna wachita chinthu choipa kwambiri.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Yehova akuti, “Uwafunse anthu a mitundu ina kuti: Kodi ndani anamvapo zinthu zofanana ndi zimenezi? Israeli amene anali ngati namwali wanga wachita chinthu choopsa kwambiri.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 18:13
14 Mawu Ofanana  

Ndipo anafika Eliyakimu, mwana wa Hilikiya, amene anali wapa nyumba, ndi Sebina, mlembi, ndi Yowa, mwana wa Asafu, mkumbutsi, kwa Hezekiya ndi zovala zao zong'ambika, namuuza iye mau a kazembeyo.


Ndani anamva kanthu kotereko? Ndani anaona zinthu zoterezo? Kodi dziko lidzabadwa tsiku limodzi? Kodi mtundu udzabadwa modzidzimutsa? Pakuti pamene Ziyoni anamva zowawa, pomwepo anabala ana ake.


Ndipo udzati kwa iwo mau awa, Maso anga agwe misozi usana ndi usiku, asaleke; pakuti namwali mwana wa anthu anga wasweka ndi kusweka kwakukulu, ndi bala lopweteka kwambiri.


Kodi matalala a Lebanoni adzalephera pamwala wa m'munda? Kodi adzaphwa madzi ozizira otsika kutali?


Mwa aneneri a ku Yerusalemu ndinaona chinthu choopsetsa; achita chigololo, ayenda monama, alimbitsa manja a ochita zoipa, ndipo palibe wobwerera kuleka zoipa zake; onse akhala kwa Ine ngati Sodomu, ndi okhalamo ake ngati Gomora.


Ndidzamangitsanso mudzi wako, ndipo udzamangidwa, iwe namwali wa Israele; udzakometsedwanso ndi mangaka, ndipo udzatulukira masewero a iwo akukondwerera.


Chodabwitsa ndi choopsa chaoneka m'dzikomo;


Ambuye wapepula ngwazi zanga zonse pakati panga; waitanira msonkhano pa ine kuti uphwanye anyamata anga, Ambuye wapondereza namwaliyo, mwana wamkazi wa Yuda, monga mopondera mphesa.


M'nyumba ya Israele ndinaona chinthu choopsetsa; pamenepo pali uhule wa Efuremu; Israele wadetsedwa.


Tamverani mau awa ndinenawa, akhalire inu nyimbo ya maliro, nyumba ya Israele inu.


Namwali wa Israele wagwa, sadzaukanso; wagwetsedwa pa nthaka yake, palibe womuutsa.


Kwamveka ndithu kuti kuli chigololo pakati panu, ndipo chigololo chotere chonga sichimveka mwa amitundu, kuti wina ali naye mkazi wa atate wake.


Ndipo Afilisti anaopa, pakuti anati, Mulungu wafika kuzithando. Ndipo iwo anati, Tsoka kwa ife! Popeza nkale lonse panalibe chinthu chotere.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa