Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 18:11 - Buku Lopatulika

11 Tsopano nenatu kwa anthu a Yuda, ndi kwa okhala m'Yerusalemu, kuti, Atero Yehova: Taonani, Ine ndipangira inu choipa, ndilingalira inu kanthu kakuchitira inu choipa; mubwerere tsono inu nonse, yense kunjira yake yoipa, nimukonze njira zanu ndi machitidwe anu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Tsopano nenatu kwa anthu a Yuda, ndi kwa okhala m'Yerusalemu, kuti, Atero Yehova: Taonani, Ine ndipangira inu choipa, ndilingalira inu kanthu kakuchitira inu choipa; mubwerere tsono inu nonse, yense kunjira yake yoipa, nimukonze njira zanu ndi machitidwe anu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Pita tsono, ukauze anthu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu kuti Chauta akuti, Ine ndikukonzekera zoti ndikuchiteni, ndikuganiza zoti ndikulangeni. Bwererani nonse, aliyense aleke njira zake zoipa. Konzani makhalidwe anu ndi zochita zanu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 “Ndipo tsopano kawawuze anthu a ku Yuda ndi amene akukhala mu Yerusalemu kuti, ‘Yehova akuti, Taonani! Ndikukukonzerani mavuto, ndi kuganizira zoti ndikulangeni. Kotero siyani makhalidwe anu oyipa aliyense wa inu, ndipo mukonzenso makhalidwe anu ndi zochita zanu.’

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 18:11
40 Mawu Ofanana  

Tiyeni, titsike, pomwepo tisokoneze chinenedwe chao, kuti wina asamvere chinenedwe cha mnzake.


Ndipo tsopano taonani, Yehova waika mzimu wonama m'kamwa mwa aneneri anu onse awa, ndipo Yehova ananena choipa cha inu.


Ndipo Yehova anachitira umboni Israele ndi Yuda mwa dzanja la mneneri aliyense, ndi mlauli aliyense, ndi kuti, Bwererani kuleka ntchito zanu zoipa, nimusunge malamulo anga ndi malemba anga, monga mwa chilamulo chonse ndinachilamulira makolo anu, ndi kuchitumizira inu mwa dzanja la atumiki anga aneneri.


Mukani, funsirani ine, ndi anthu, ndi Yuda yense, kwa Yehova za mau a buku ili adalipeza; pakuti mkwiyo wa Yehova wotiyakira ife ndi waukulu; popeza atate athu sanamvere mau a buku ili, kuchita monga mwa zonse zotilemberamo.


Pamenepo mfumu ya Aramu inati, Tiye, muka, ndidzatumiza kalata kwa mfumu ya Israele. Pamenepo anachoka, atatenga siliva matalente khumi, ndi golide masekeli zikwi zisanu ndi chimodzi, ndi zovala zakusintha khumi.


Ndipo tsopano ndidzakuuzani chimene nditi ndichite ndi munda wanga wampesa; ndidzachotsapo tchinga lake, ndipo zidzadyedwa; ndidzagumula linga lake ndipo zidzapondedwa pansi;


Wolungama atayika, ndipo palibe munthu wosamalirapo; ndipo anthu achifundo atengedwa, palibe wolingalira kuti wolungama achotsedwa pa choipa chilinkudza.


Chifukwa chake atero Yehova, Taonani, ndidzatengera pa iwo choipa, chimene sangathe kuchipulumuka; ndipo adzandifuulira Ine, koma sindidzamvera iwo.


Koma ine ndinanga mwanawankhosa wofatsa wotengedwa kukaphedwa; ndipo sindinadziwe kuti anandichitira ine chiwembu, kuti, Tiononge mtengo ndi zipatso zake, timdule iye padziko la amoyo, kuti dzina lake lisakumbukikenso.


Ndipo iwo anati, Tiyeni, tilingalire Yeremiya chomchitira choipa; pakuti chilamulo sichidzathera wansembe, kapena uphungu wanzeru, kapena mau mneneri. Tiyeni, timpande iye ndi lilime, tisamvere iye mau ake ali onse.


Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele atero, Taonani, ndidzatengera mzinda uwu ndi midzi yake yonse choipa chonse chimene ndaunenera; chifukwa anaumitsa khosi lao, kuti asamve mau anga.


nuti, Tamvani mau a Yehova, inu mafumu a Yuda, ndi okhala mu Yerusalemu; Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele atero, Taonani, ndidzatengera malo ano choipa, chimene aliyense adzachimva, makutu ake adzachita woo.


amene mneneri Yeremiya ananena kwa anthu onse a Yuda, ndi onse okhala mu Yerusalemu, kuti,


ndi kuti, Mubwerere tsopano nonsenu, yense kuleka njira yake yoipa, ndi zoipa za ntchito zanu, ndi kukhala m'dziko limene Yehova anapatsa inu ndi makolo anu, kuyambira kale kufikira muyaya;


Chifukwa chake tsopano konzani njira zanu ndi machitidwe anu, ndi kumvera mau a Yehova Mulungu wanu; ndipo Yehova adzaleka choipa chimene ananenera inu.


Kapena adzamvera, nadzatembenuka, yense kusiya njira yake yoipa; kuti ndileke choipa, chimene ndinati ndiwachitire chifukwa cha kuipa kwa ntchito zao.


Amati, Ngati mwamuna achotsa mkazi wake, ndipo amchokera iye, nakhala mkazi wa wina, kodi adzabweranso kwa mkaziyo? Dzikolo kodi silidzaipitsidwa? Koma iwe wachita dama ndi mabwenzi ambiri; koma bweranso kwa Ine, ati Yehova.


Bwerani, ana inu obwerera, ndidzachiritsa mabwerero anu. Taonani, tadza kwa Inu; pakuti ndinu Yehova Mulungu wathu.


Ndatumanso kwa inu atumiki anga onse aneneri, ndalawirira ndi kuwatuma, kuti, Bwererani kuleka yense njira yake yoipa, konzani machitidwe anu, musatsate milungu ina kuitumikira, ndipo mudzakhala m'dziko limene ndakupatsani inu ndi makolo anu; koma simunanditchere khutu lanu, simunandimvere Ine.


Kapena nyumba ya Yuda idzamva choipa chonse chimene nditi ndidzawachitire; kuti abwerere yense kuleka njira yake yoipa; kuti ndikhululukire mphulupulu yao ndi tchimo lao.


Kapena pembedzero lao lidzagwa pamaso pa Yehova, ndipo adzabwerera yense kuleka njira yake yoipa; pakuti mkwiyo ndi ukali umene Yehova wanenera anthu awa ndi waukulu.


Ngati udzabwera, Israele, ati Yehova, udzabwera kwa Ine; ndipo ngati udzachotsa zonyansa zako pamaso panga sudzachotsedwa.


Iwe Yerusalemu, utsuke mtima wako kuchotsa zoipa kuti upulumuke. Maganizo ako achabe agona mwako masiku angati?


Ndinaona dziko lapansi, ndipo taona, linali lopasuka lopanda kanthu; ndipo ndinaona kumwamba, kunalibe kuunika.


Kwezani mbendera kuyang'ana ku Ziyoni; thawani kuti mupulumuke, musakhale; pakuti ndidza ndi choipa chochokera kumpoto ndi kuononga kwakukulu.


Nolani mivi; gwirani zolimba zikopa; Yehova waukitsa mtima wa mafumu a Amedi; chifukwa alingalirira Babiloni kuti amuononge; pakuti ndi kubwezera chilango kwa Yehova; kubwezera chilango chifukwa cha Kachisi wake.


Yehova wa makamu atero, Mulungu wa Israele, Konzani njira zanu ndi machitidwe anu, ndipo ndidzakukhalitsani inu m'malo ano.


Popeza mwamvetsa chisoni ndi mabodza mtima wa wolungama, amene sindinamvetse chisoni Ine, ndi kumlimbitsa manja woipa, kuti asabwerere kuleka njira yake yoipa, ndi kusungidwa wamoyo;


Ngati ndikondwera nayo imfa ya woipa? Ati Ambuye Yehova, si ndiko kuti abwerere kuleka njira yake, ndi kukhala ndi moyo?


koma zifundidwe ndi chiguduli munthu ndi nyama, ndipo zifuulire kolimba kwa Mulungu; ndipo abwere yense kuleka njira yake yoipa, ndi chiwawa chili m'manja mwake.


Chifukwa chake atero Yehova, Taonani, ndilingirira choipa pa banja ili, chimene simudzachotsako makosi anu, kapena kuyenda modzikuza inu; pakuti nyengo iyi ndi yoipa.


Chifukwa chake uziti nao, Atero Yehova wa makamu: Bwererani kudza kwa Ine, ati Yehova wa makamu, ndipo Ine ndidzabwerera kudza kwa inu, ati Yehova wa makamu.


komatu kuyambira kwa iwo a mu Damasiko, ndi a mu Yerusalemu, ndi m'dziko lonse la Yudeya, ndi kwa amitundunso ndinalalikira kuti alape, natembenukire kwa Mulungu, ndi kuchita ntchito zoyenera kutembenuka mtima.


Nanga tsono, inu akunena, Lero kapena mawa tidzapita kulowa kumudzi wakutiwakuti, ndipo tidzagonerako ndi kutsatsa malonda, ndi kupindula nao;


Nanga tsono achuma inu, lirani ndi kuchema chifukwa cha masautso anu akudza pa inu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa