Yeremiya 18:10 - Buku Lopatulika10 koma ukachita choipa pamaso panga, osamvera mau anga, pamenepo ndidzaleka chabwinocho, ndidati ndiwachitire. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201410 koma ukachita choipa pamaso panga, osamvera mau anga, pamenepo ndidzaleka chabwinocho, ndidati ndiwachitire. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa10 koma mtunduwo nkumapitiriza kuchita zoipa pamaso panga, osamvera mau anga, ndiye kuti sindidzauchitira zabwino zimene ndidaati ndiwuchitire. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero10 Koma mtunduwo ukachita choyipa pamaso panga nʼkusandimvera, ndiye kuti sindidzawuchitiranso zabwino zimene ndimafuna ndiwuchitire. Onani mutuwo |
Koma wolungamayo akabwerera kuleka chilungamo chake, nakachita mphulupulu, ndi kuchita monga mwa zonyansa zonse azichita woipa, adzakhala ndi moyo kodi? Nnena chimodzi cha zolungama zake zonse adzazichita chidzakumbukika m'kulakwa kwake analakwa nako, ndi m'kuchimwa kwake anachimwa nako; momwemo adzafa.
Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, unene ndi ana a anthu a mtundu wako, Cholungama cha wolungama sichidzamlanditsa tsiku la kulakwa kwake, ndi kunena za choipa cha woipa, sadzagwa nacho tsiku lakubwerera iye kuleka choipa chake; ndi munthu wolungama sadzakhoza kukhala ndi moyo ndi chilungamo chake tsiku lakuchimwa iye.