Yeremiya 17:8 - Buku Lopatulika8 Ndipo adzakhala ngati mtengo wooka kuli madzi, wotambalitsa mizu yake pamtsinje, wosaopa pofika nyengo yadzuwa, koma tsamba lake likhala laliwisi; ndipo suvutika chaka cha chilala, suleka kubala zipatso. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20148 Ndipo adzakhala ngati mtengo wooka kuli madzi, wotambalitsa mizu yake pamtsinje, wosaopa pofika nyengo yadzuwa, koma tsamba lake likhala laliwiri; ndipo suvutika chaka cha chilala, suleka kubala zipatso. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa8 Adzakhala ngati mtengo wobzalidwa m'mphepete mwa mtsinje, umene umatambalitsa mizu yake m'mbali mwa madzi. Suwopa kukamatentha, chifukwa masamba ake safota. Pa chaka chachilala sukuda nkhaŵa, ndipo suleka kubala zipatso.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero8 Adzakhala ngati mtengo wodzalidwa mʼmphepete mwa madzi umene umatambalitsa mizu yake mʼmbali mwa mtsinje. Mtengowo suopa pamene kukutentha; masamba ake amakhala obiriwira nthawi zonse. Suchita mantha pa chaka cha chilala ndipo sulephera kubereka chipatso.” Onani mutuwo |