Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 17:6 - Buku Lopatulika

6 Ndipo adzakhala ngati tsanya la m'chipululu, ndipo saona pamene chifika chabwino; koma adzakhala m'malo oumitsa m'chipululu, dziko lachikungu lopanda anthu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Ndipo adzakhala ngati tsanya la m'chipululu, ndipo saona pamene chifika chabwino; koma adzakhala m'malo oumitsa m'chipululu, dziko lachikungu lopanda anthu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Woteroyo adzakhala ngati chitsamba m'chipululu, ndipo sadzapeza zabwino. Adzakhala m'chipululu mopanda madzi, m'dziko lamchere m'mene anthu sangathe kukhalamo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Munthuyo adzakhala ngati chitsamba mʼchipululu; iye sadzapeza zabwino. Adzakhala mʼchipululu mopanda madzi, mʼdziko lamchere limene munthu sangathe kukhalamo.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 17:6
17 Mawu Ofanana  

Pamenepo kazembe amene mfumu ankatsamira padzanja lake anamyankha munthu wa Mulungu, nati, Taonani, Yehova angachite mazenera m'mwamba chidzachitika ichi kodi? Nati iye, Taona, udzachiona ndi maso ako, koma iwe sudzadyako ai.


Sadzapenyerera timitsinje, toyenda nao uchi ndi mafuta.


imene ndachiyesa chipululu nyumba yake, ndi dziko lakhulo pokhala pake?


Oipa satero ai; koma akunga mungu wouluka ndi mphepo.


Dziko la zipatso, likhale lakhulo, chifukwa cha choipa cha iwo okhalamo.


chakuti pophuka oipa ngati msipu, ndi popindula ochita zopanda pake; chitero kuti adzaonongeke kosatha.


Chifukwa mudzakhala ngati mtengo wathundu, umene tsamba lake linyala, ngatinso munda wopanda madzi.


chifukwa chake atero Yehova, Taonani, ndidzalanga Semaya Mnehelamu, ndi mbeu zake; sadzakhala ndi munthu wakukhala mwa anthu awa, sadzaona zabwino ndidzachitira anthu anga, ati Yehova: chifukwa wanena zopikisana ndi Yehova.


Thawani, pulumutsani miyoyo yanu, mukhale amaliseche m'chipululu.


Koma pali matope ake ndi zithaphwi zake sipadzakonzeka, paperekedwa pakhale pamchere.


Chifukwa chake, pali moyo wanga, ati Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, Zedi Mowabu adzakhala ngati Sodomu, ndi ana a Amoni ngati Gomora, pochuluka khwisa ndi maenje a mchere, ndi bwinja losatha; otsala a anthu anga adzalanda zao, ndi otsala a mtundu wa anthu anga adzawalandira akhale cholowa chao.


Ndi kuti lidapsa dziko lake lonse ndi sulufure, ndi mchere, kuti sabzalamo, kapena siliphukitsa kanthu kapena sumerapo msipu, monga kupasula kwake kwa Sodomu ndi Gomora, Adima, ndi Zeboimu, imene Yehova anaipasula m'mkwiyo wake ndi ukali wake;


Ndipo Abimeleki analimbana ndi mzinda tsiku lija lonse; nalanda mzinda nawapha anthu anali m'mwemo; napasula mzinda; nawazapo mchere.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa