Yeremiya 17:26 - Buku Lopatulika26 Ndipo adzachokera kumizinda ya Yuda, ndi kumalo akuzungulira Yerusalemu, ndi kudziko la Benjamini, ndi kuchidikha, ndi kumapiri, ndi kumwera, ndi kudza nazo nsembe zopsereza, ndi nsembe zophera, ndi nsembe zaufa, ndi lubani, ndi kudza nazo zamayamikiro, kunyumba ya Yehova. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201426 Ndipo adzachokera kumidzi ya Yuda, ndi kumalo akuzungulira Yerusalemu, ndi kudziko la Benjamini, ndi kuchidikha, ndi kumapiri, ndi kumwera, ndi kudza nazo nsembe zopsereza, ndi nsembe zophera, ndi nsembe zaufa, ndi lubani, ndi kudza nazo zamayamikiro, kunyumba ya Yehova. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa26 Anthu adzachokera ku mizinda ya Yuda ndi dziko lonse lozungulira Yerusalemu, dziko la Benjamini, dziko lazidikha, dziko lazitunda, ndiponso ku Negebu, atatenga nsembe zopsereza, nsembe zaufa, nsembe zalubani, ndiponso nsembe zothokozera, kupita nazo ku Nyumba ya Chauta. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero26 Anthu adzabwera kuchokera ku mizinda ya Yuda ndi ku midzi yozungulira Yerusalemu, kuchokera ku dziko la Benjamini ndi ku mapiri a kumadzulo, kuchokera ku dziko la mapiri ndi ku Negevi. Adzabwera ndi nsembe zopsereza, nsembe zaufa ndi za chakudya, nsembe za lubani ndi zopereka zachiyamiko ku nyumba ya Yehova. Onani mutuwo |
Anthu adzagula minda ndi ndalama, adzalembera makalata ogulira, adzawasindikiza, adzaitana mboni, m'dziko la Benjamini, ndi m'malo ozungulira Yerusalemu, ndi m'mizinda ya Yuda, ndi m'mizinda ya kumtunda, ndi m'mizinda ya kuchidikha, ndi m'mizinda ya kumwera; pakuti ndidzabweza undende wao, ati Yehova.
mudzamvekanso mau akukondwa ndi mau akusekera, mau a mkwati ndi mau a mkwatibwi, mau a iwo akuti, Myamikireni Yehova wa makamu, pakuti Yehova ndiye wabwino, chifundo chake nchosatha; ndi a iwo akutengera nsembe zoyamikira m'nyumba ya Yehova. Pakuti ndidzabweza undende wa dziko monga poyamba, ati Yehova.