Yeremiya 17:25 - Buku Lopatulika25 pamenepo padzalowa pa zipata za mzinda uwu mafumu ndi akulu okhala pa mpando wachifumu wa Davide, okwera pa magaleta ndi akavalo, iwo, ndi akulu ao, anthu a Yuda, ndi okhala mu Yerusalemu; ndipo mzinda uwu udzakhala kunthawi zamuyaya. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201425 pamenepo padzalowa pa zipata za mudzi uwu mafumu ndi akulu okhala pa mpando wachifumu wa Davide, okwera pa magaleta ndi akavalo, iwo, ndi akulu ao, anthu a Yuda, ndi okhala m'Yerusalemu; ndipo mudzi uwu udzakhala kunthawi zamuyaya. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa25 Mukatsata zimenezi, ndiye kuti pa zipata za mzinda umenewu pazidzaloŵera mafumu odzakhala pa mpando waufumu wa Davide. Azidzaloŵa atakwera pa magareta ndi pa akavalo, ali pamodzi ndi akalonga ao ndi anthu a ku Yuda ndiponso anthu a mu Yerusalemu. Ndipo anthu adzakhazikika mu mzinda umenewu mpaka muyaya. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero25 Mukatero ndiye mafumu anu amene akukhala pa mpando wa Davide adzatulukira pa zipata za mzindawu pamodzi ndi nduna zawo. Iwo pamodzi ndi nduna zawo azidzalowa atakwera magaleta ndi akavalo, akuperekezedwa ndi anthu a ku Yuda ndi amene amakhala mu Yerusalemu, ndipo mu mzinda muno mudzakhala anthu mpaka muyaya. Onani mutuwo |