Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 17:21 - Buku Lopatulika

21 atero Yehova: Tadzayang'anirani nokha, musanyamule katundu tsiku la Sabata, musalowe naye pa zipata za Yerusalemu;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

21 atero Yehova: Tadzayang'anirani nokha, musanyamule katundu tsiku la Sabata, musalowe naye pa zipata za Yerusalemu;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

21 M'mau a Chautawo ndi aŵa: Kuti musunge moyo wanu, samalani bwino kuti pa tsiku la Sabata musanyamule katundu, kapena kuloŵa naye pa zipata za Yerusalemu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

21 Yehova akuti: samalani kuti pa tsiku la Sabata musanyamule katundu kapena kulowa naye pa zipata za Yerusalemu.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 17:21
18 Mawu Ofanana  

Udzikumbukira tsiku la Sabata, likhale lopatulika.


Chinjiriza mtima wako koposa zonse uzisunga; pakuti magwero a moyo atulukamo.


Wodala munthu amene achita ichi, ndi mwana wa munthu amene agwira zolimba ichi, amene asunga Sabata osaliipitsa, nasunga dzanja lake osachita nalo choipa chilichonse.


Ukaletsa phazi lako pa Sabata, ndi kusiya kuchita kukondwerera kwako tsiku langa lopatulika, ndi kuyesa Sabata tsiku lokondwa lopatulika la Yehova, lolemekezeka, ndipo ukalilemekeza ilo, osachita njira zako zokha, osafuna kukondwa kwako kokha, osalankhula mau ako okha;


Ndipo ananena nao, Yang'anirani chimene mukumva; ndi muyeso umene muyesera nao udzayesedwa kwa inu; ndipo kudzaonjezedwa kwa inu.


Chifukwa chake yang'anirani mamvedwe anu; pakuti kudzapatsidwa kwa iye amene ali nacho; ndipo kwa iye amene alibe chidzachotsedwa, chingakhale chija aoneka ngati ali nacho.


Tadzichenjerani nokha, ndi gulu lonse, pamenepo Mzimu Woyera anakuikani oyang'anira, kuti muwete Mpingo wa Mulungu, umene anaugula ndi mwazi wa Iye yekha.


Dzichenjerani nokha, angachete mitima yanu, nimungapatuke, ndi kutumikira milungu ina, ndi kuipembedza;


Potero dzichenjerani nao moyo wanu ndithu; popeza simunapenye mafanidwe konse tsikuli Yehova ananena ndi inu mu Horebu, ali pakati pa moto;


Dzichenjerani, mungaiwale chipangano cha Yehova Mulungu wanu, chimene anapangana nanu, ndi kuti mungadzipangire fano losema, chifaniziro cha kanthu kalikonse Yehova Mulungu wanu anakuletsani.


Chokhachi, dzichenjerani nokha, ndi kusunga moyo wanu mwachangu, kuti mungaiwale zinthuzi adaziona maso anu, ndi kuti zisachoke kumtima kwanu masiku onse a moyo wanu; koma muzidziwitsa ana anu ndi zidzukulu zanu.


Potero mudzisamalire ndithu kuti mukonde Yehova Mulungu wanu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa