Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 17:16 - Buku Lopatulika

16 Koma ine, pokhala mbusa sindinafulumire kuchokerako kuti ndikutsateni Inu; sindinakhumbe tsiku la tsoka; Inu mudziwa, chimene chinatuluka pa milomo yanga chinali pamaso panu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Koma ine, pokhala mbusa sindinafulumira kuchokerako kuti ndikutsateni Inu; sindinakhumba tsiku la tsoka; Inu mudziwa, chimene chinatuluka pa milomo yanga chinali pamaso panu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Ine sindidakukakamizeni kuti mufikitse zovuta. Mukudziŵa kuti tsiku la tsoka sindinkalilakalaka. Zonse zimene ndidalankhula mukuzidziŵa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Ine sindinakuwumirizeni kuti muwalange. Mukudziwa kuti ine sindilakalaka tsiku la tsoka. Zonse zimene ndinayankhula Inu mukuzidziwa.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 17:16
21 Mawu Ofanana  

Koma inu, Yehova, mundidziwa ine; mundiona ine, muyesa mtima wanga ngati utani nanu; muwatulutse iwo monga nkhosa za kuphedwa, ndi kuwakonzeratu tsiku lakuphedwa.


Koma ngati simudzamva, moyo wanga udzalira m'tseri chifukwa cha kunyada kwanu; diso langa lidzalira kwambiri, lidzagwa misozi, chifukwa zoweta za Yehova zagwidwa m'nsinga.


Inu Yehova, mudziwa; mundikumbukire ine, mundiyang'anire Ine, mundibwezere chilango pa ondisautsa ine; musandichotse m'chipiriro chanu; dziwani kuti chifukwa cha Inu ndanyozedwa.


Kodi choipa chibwezedwe pa chabwino? Pakuti akumbira moyo wanga dzenje. Mukumbukire kuti ndinaima pamaso panu kuwanenera zabwino, kuwachotsera iwo ukali wanu.


Yehova, mwandikopa ine, ndipo ndinakopedwa; muli ndi mphamvu koposa ine, ndipo mwapambana; ine ndikhala choseketsa dzuwa lonse, onse andiseka.


Ndipo ngati nditi, Sindidzamtchula Iye, sindidzanenanso m'dzina lake, pamenepo m'mtima mwanga muli ngati moto wotentha wotsekedwa m'mafupa anga, ndipo ndalema ndi kupirira, sindingathe kupiriranso.


Ha, mutu wanga ukadakhala madzi, ndi maso anga kasupe wa misozi, kuti usana ndi usiku ndilirire ophedwa a mwana wamkazi wa anthu anga!


Iwo adana naye wodzudzula kuchipata, nanyansidwa naye wolunjikitsa mau.


kuti sindinakubisirani zinthu zopindulira, osazilalikira kwa inu, ndi kukuphunzitsani inu pabwalo ndi m'nyumba zanu,


Pakuti sindinakubisirani pakukulalikirani uphungu wonse wa Mulungu.


Pakuti kudzitamandira kwathu ndiko umboni wa chikumbumtima chathu, kuti m'chiyero ndi kuona mtima kwa Mulungu, si m'nzeru ya thupi, koma m'chisomo cha Mulungu tinadzisunga m'dziko lapansi, koma koposa kwa inu.


Pakuti sitikhala monga ambiriwo, akuchita malonda nao mau a Mulungu; koma monga mwa choona mtima, koma monga mwa Mulungu pamaso pa Mulungu, tilankhula mwa Khristu.


Mudziwa, abale anga okondedwa, kuti munthu aliyense akhale wotchera khutu, wodekha polankhula, wodekha pakupsa mtima.


Musakhale aphunzitsi ambiri, abale anga, podziwa kuti tidzalangika koposa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa