Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 16:6 - Buku Lopatulika

6 Akulu ndi ang'onong'ono adzafa m'dziko muno; sadzaikidwa, anthu sadzachita maliro ao, sadzadzicheka, sadzadziyeseza adazi, chifukwa cha iwo;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Akulu ndi ang'onong'ono adzafa m'dziko muno; sadzaikidwa, anthu sadzachita maliro ao, sadzadzicheka, sadzadziyeseza adazi, chifukwa cha iwo;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Akuluakulu ndi ang'onoang'ono omwe, onsewo adzafa m'dziko lino. Koma maliro ao sadzaikidwa, iwowo sadzaŵalira. Palibe amene adzaonetse chisoni podzichekacheka kapena kumeta tsitsi chifukwa cha malirowo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Akuluakulu ndi angʼonoangʼono omwe adzafa mʼdziko muno. Sadzayikidwa mʼmanda kapena kuliridwa, ndipo palibe amene adzaonetse chisoni podzichekacheka kapena kumeta tsitsi lake chifukwa cha iwo.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 16:6
20 Mawu Ofanana  

Pakuti Iye anawakweretsera mfumu ya Ababiloni, ndiye anawaphera anyamata ao ndi lupanga, m'nyumba ya malo ao opatulika, osachitira chifundo mnyamata kapena namwali, mkulu kapena nkhalamba; Mulungu anawapereka onse m'dzanja lake.


Ndipo tsiku limenelo Ambuye, Yehova wa makamu, anaitana kulira, ndi kugwa misozi, ndi kumeta, ndi kuvala chiguduli m'chuuno;


Ndipo padzakhala monga ndi anthu, moteronso ndi ansembe; monga ndi mtumiki, moteronso ndi mbuyake; monga ndi mdzakazi, moteronso ndi mbuyake wamkazi; monga ndi wogula, moteronso ndi wogulitsa; monga ndi wobwereka, moteronso ndi wombwereka; monga ndi wotenga phindu, moteronso ndi wombwezera phindu kwa iye.


Ndipo udzati kwa iwo, Atero Yehova, Taonani, ndidzadzaza ndi chiledzero onse okhala m'dziko muno, ngakhale mafumu onse amene akhala pa mpando wachifumu wa Davide, ndi ansembe, ndi aneneri, ndi onse okhala mu Yerusalemu.


Adzafa ndi imfa zanthenda; sadzaliridwa maliro, sadzaikidwa; adzakhala ngati ndowe panthaka; ndipo adzathedwa lupanga, ndi njala; ndipo mitembo yao idzakhala chakudya cha mbalame za kumlengalenga, ndi zilombo za dziko lapansi.


anadza anthu ochokera ku Sekemu, ndi ku Silo, ndi ku Samariya, anthu makumi asanu ndi atatu, atameta ndevu zao, atang'amba zovala zao, atadzitematema, anatenga nsembe zaufa ndi lubani m'manja mwao, kunka nazo kunyumba ya Yehova.


Dazi lafikira a Gaza; Asikeloni wathedwa, otsala m'chidikha chao; udzadzicheka masiku angati?


Pakuti mitu yonse ili yadazi, ndipo ndevu zili zometedwa; pa manja onse pali pochekedwachekedwa, ndi pachiuno chiguduli.


Meta tsitsi lako, iwe Yerusalemu, nulitaye, nukweze maliro pa mapiri oti see; pakuti Yehova wakana ndi kusiya mbadwo umene aukwiyira.


ndipo udzawayanika padzuwa, ndi pamwezi, ndi pa khamu lonse la kuthambo, limene analikonda, ndi kulitumikira, ndi kulitsata, ndi kulifuna, ndi kuligwadira; sadzasonkhanidwa, sadzaikidwa; adzakhala ndowe panthaka.


Musamameta mduliro, kapena kumeta m'mphepete mwa ndevu zanu.


Musamadzicheka matupi anu chifukwa cha akufa, kapena kutema mphini; Ine ndine Yehova.


Pakuti taonani, Yehova walamulira, nadzakantha nyumba yaikulu ichite mpata, ndi nyumba yaing'ono ichite mindala.


Ndipo Yesu polowa m'nyumba yake ya mkuluyo, ndi poona oimba zitoliro ndi khamu la anthu obuma,


Inu ndinu ana a Yehova Mulungu wanu; musamadzicheka, kapena kumeta tsitsi pakati pamaso chifukwa cha akufa.


Ndipo ndinaona akufa, aakulu ndi aang'ono alinkuima kumpando wachifumu; ndipo mabuku anatsegulidwa; ndipo buku lina linatsegulidwa, ndilo la moyo; ndipo akufa anaweruzidwa mwa zolembedwa m'mabuku, monga mwa ntchito zao.


Ndipo mafumu a dziko, ndi akulu, ndi akazembe, ndi achuma, ndi amphamvu, ndi akapolo onse, ndi mfulu, anabisala kumapanga, ndi matanthwe a mapiri;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa