Yeremiya 16:16 - Buku Lopatulika16 Taonani, ndidzaitana akugwira nsomba ambiri, ati Yehova, ndipo adzawagwira iwo, pambuyo pake ndidzaitana osaka nyama ambiri, ndipo adzasaka iwo m'mapiri onse, ndi pa zitunda zonse, ndiponso m'mapanga a m'matanthwe. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201416 Taonani, ndidzaitana akugwira nsomba ambiri, ati Yehova, ndipo adzawagwira iwo, pambuyo pake ndidzaitana osaka nyama ambiri, ndipo adzasaka iwo m'mapiri onse, ndi pa zitunda zonse, ndiponso m'mapanga a m'matanthwe. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa16 Chauta akuti, “Ndidzaitana adani ambiri okhala ngati asodzi a nsomba, ndipo adzaŵagwira anthuŵa ngati nsomba. Pambuyo pake ndidzaitana adani enanso ambiri okhala ngati alenje, kuti akaŵasake anthuŵa ku mapiri, ku zitunda, ndiponso m'mapanga am'matanthwe. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero16 Yehova akuti, “Koma tsopano ndidzayitana adani okhala ngati asodzi ambiri, ndipo adzawagwira ngati nsomba. Izi zitatha adani enanso okhala ngati alenje ambiri, adzawasaka pa phiri lililonse, pa chitunda chilichonse ndiponso mʼmapanga onse a mʼmatanthwe. Onani mutuwo |
taonani, Ine, ndidzatuma ndi kutenga mabanja onse a kumpoto, ati Yehova, ndipo ndidzatuma kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, mtumiki wanga, ndipo ndidzatengera iwo padziko lino, ndi pa okhalamo ake onse, ndi pa mitundu iyi yozungulira, ndipo ndidzathetsa iwo ndithu, ndi kuwayesa iwo chizizwitso, ndi chotsonyetsa, ndi bwinja lamuyaya.