Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 16:13 - Buku Lopatulika

13 chifukwa chake ndidzakutulutsani inu m'dziko muno munke kudziko limene simunadziwa, kapena inu kapena makolo anu; pamenepo mudzatumikira milungu ina usana ndi usiku, kumene sindidzachitira inu chifundo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 chifukwa chake ndidzakutulutsani inu m'dziko muno munke kudziko limene simunadziwa, kapena inu kapena makolo anu; pamenepo mudzatumikira milungu ina usana ndi usiku, kumene sindidzachitira inu chifundo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Motero Ine ndidzakupirikitsani m'dziko lino ndi kukuloŵetsani m'dziko limene inu ndi makolo anu simulidziŵa. Kumeneko mudzatumikira milungu ina usana ndi usiku, chifukwa Ine sindidzakuchitiraninso chifundo.’ ”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Choncho Ine ndidzakubalalitsani mʼdziko muno ndi kukulowetsani mʼdziko limene inu ndi makolo anu simunalidziwe. Kumeneko mukatumikira milungu ina usana ndi usiku, ndipo sadzakuchitirani chifundo.’ ”

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 16:13
21 Mawu Ofanana  

Niwakantha mfumu ya Babiloni, niwaphera ku Ribula m'dziko la Hamati. Motero anamuka nao Ayuda andende kuwachotsa m'dziko lao.


pamenepo ndidzawazula m'dziko langa limene ndinawapatsa; ndi nyumba ino ndinaipatulira dzina langa ndidzaitaya, osaionanso, ndi kuiyesa mwambi ndi mnyozo mwa mitundu yonse ya anthu.


Potero ndinawaperekera kuuma mtima kwao, ayende monga mwa uphungu waowao.


Pakuti atero Yehova, Taonani, ndidzaponya kunja okhala m'dziko ili tsopanoli, ndi kuwasautsa, kuti azindikire.


Inu, chiyembekezo cha Israele, Mpulumutsi wake nthawi ya msauko, bwanji mukhala ngati mlendo m'dziko, ngati woyendayenda amene apatuka usiku?


Ndipo Yehova anati kwa ine, Ngakhale Mose ndi Samuele akadaima pamaso panga, koma mtima wanga sukadasamalira anthu awa; muwachotse iwo pamaso panga, atuluke.


Ndipo ndidzawapititsa iwo pamodzi ndi adani ako kudziko limene sudziwa iwe; pakuti moto wayaka m'mkwiyo wanga, umene udzatentha inu.


Ndipo ndidzawapereka akhale oopsetsa m'maufumu onse a dziko lapansi, chifukwa cha Manase mwana wa Hezekiya mfumu ya Yuda, chifukwa cha zija anachita mu Yerusalemu.


Pakuti Yehova atero, Usalowe m'nyumba ya maliro, usanke kukachita maliro ao, kapena kuwalirira; pakuti ndachotsa mtendere wanga pa anthu awa, chifundo ndi nsoni zokoma, ati Yehova.


Iwe, iwe wekha, udzaleka pa cholowa chako chimene ndinakupatsa iwe; ndipo ndidzakutumikiritsa adani ako m'dziko limene sulidziwa; pakuti wakoleza moto m'mkwiyo wanga umene udzatentha kunthawi zamuyaya.


Ndipo ndidzakutulutsa iwe, ndi mai wako wakubala iwe, kulowa m'dziko lina, limene sunabadwiremo; m'menemo udzafa.


Kodi munthu uyu Koniya ndiye mbiya yopepuka yosweka? Kodi ndiye mbiya yosakondweretsa? Chifukwa chanji atulutsidwa iye, ndi mbeu zake, ndi kuponyedwa m'dziko limene salidziwa?


Ndipo padzakhala pamene mudzati, Chifukwa chanji Yehova Mulungu wathu atichitira ife zonse izi? Ndipo udzayankha kwa iwo, Monga ngati mwandisiya Ine, ndi kutumikira milungu yachilendo m'dziko lanu, momwemo mudzatumikira alendo m'dziko silili lanu.


Kodi anakhala ndi manyazi pamene anachita chonyansa? Iai, sanakhale konse ndi manyazi, sanathe kunyala; chifukwa chake adzagwa mwa iwo akugwa; panthawi pamene ndidzafika kwa iwo, adzagwetsedwa, ati Yehova.


Yehova adzamukitsa inu, ndi mfumu yanu imene mudzadziikira, kwa mtundu wa anthu umene simuudziwa, inu kapena makolo anu; ndipo mudzatumikirako milungu ina ya mitengo ndi miyala.


Ndipo Yehova anawazula m'nthaka mwao mokwiya ndi mozaza, ndi mu ukali waukulu, nawaponya m'dziko lina, monga lero lino.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa