Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 15:18 - Buku Lopatulika

18 Kupweteka kwanga kuli chipwetekere bwanji, ndi bala langa losapoleka, likana kupola? Kodi mudzakhala kwa ine ngati kamtsinje konyenga, ngati madzi omwerera?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 Kupweteka kwanga kuli chipwetekere bwanji, ndi bala langa losapoleka, likana kupola? Kodi mudzakhala kwa ine ngati kamtsinje konyenga, ngati madzi omwerera?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 Nanga chifukwa chiyani mavuto anga sakutha? Chilonda changa nchosatha, sichikupola. Monga nkuti mwandinyenga ngati chitsime chouma kapena ngati mtsinje wopanda madzi?”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 Nanga nʼchifukwa chiyani mavuto anga sakutha? Bwanji chilonda changa sichikupola? Kodi inu mudzakhala ngati mtsinje wowuma nthawi yachilimwe, kapena ngati kasupe wopanda madzi?”

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 15:18
15 Mawu Ofanana  

Madzi achoka m'nyanja, ndi mtsinje ukuphwa, nuuma;


Kodi ndidzinamizire? Bala langa nlosapola, ngakhale sindinalakwe.


Moyo wanganso wanthunthumira kwakukulu; ndipo Inu, Yehova, kufikira liti?


Kodi mwakanadi Yuda? Kodi mtima wanu wanyansidwa ndi Ziyoni? Bwanji mwatipanda ife, ndipo tilibe kuchira? Tinayembekeza mtendere, koma sizinafike zabwino; tinayembekeza nthawi yakuchira, ndipo taonani mantha!


Akulu ao atuma ang'ono ao kumadzi; afika kumaenje, osapeza madzi; abwera ndi mitsuko yao yopanda kanthu; ali ndi manyazi, athedwa nzeru, afunda mitu yao.


Chifukwa chanji ndinatuluka m'mimba kuti ndione kutopa ndi kulira, kuti masiku anga athe ndi manyazi?


Yehova, mwandikopa ine, ndipo ndinakopedwa; muli ndi mphamvu koposa ine, ndipo mwapambana; ine ndikhala choseketsa dzuwa lonse, onse andiseka.


Pakuti atero Yehova, Kulaswa kwako kuli kosapoleka ndi bala lako lili lowawa.


Chifukwa chanji ulirira bala lako? Kuphwetekwa kwako kuli kosapoleka; chifukwa cha mphulupulu yako yaikulu, chifukwa zochimwa zako zinachuluka, ndakuchitira iwe izi.


Chifukwa chake pereka mphatso zolawirana kwa Moreseti-Gati; nyumba za Akizibu zidzakhala chinthu chabodza kwa mafumu a Israele.


Pakuti mabala ake ndi osapola; pakuti afikira ku Yuda; afikira ku chipata cha anthu anga, ku Yerusalemu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa