Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 14:18 - Buku Lopatulika

18 Ndikatulukira kumunda, taonani ophedwa ndi lupanga! Ndikalowa m'mzinda, taonani odwala ndi njala! Pakuti mneneri ndi wansembe ayendayenda m'dziko osadziwa kanthu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 Ndikatulukira kumunda, taonani ophedwa ndi lupanga! Ndikalowa m'mudzi, taonani odwala ndi njala! Pakuti mneneri ndi wansembe ayendayenda m'dziko osadziwa kanthu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 Ndikamayenda ku thengo, ndikuwona anthu ophedwa pa nkhondo. Ndikaloŵa mu mzinda, ndikuwona anthu ofa ndi njala. Aneneri ndi ansembe akupitirizabe ntchito zao m'dzikomo, koma osadziŵa zimene akuchita.’ ”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 Ndikapita kuthengo, ndikuona amene aphedwa ndi lupanga; ndikapita mu mzinda, ndikuona amene asakazidwa ndi njala. Ngakhale aneneri pamodzi ndi ansembe onse atengedwa.’ ”

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 14:18
19 Mawu Ofanana  

Iwe amene wadzala ndi zimfuu, mzinda waphokoso, mzinda wokondwa; ophedwa ako sanaphedwe ndi lupanga, sanafe m'nkhondo.


Koma iwonso adzandima ndi vinyo, nasochera ndi chakumwa chaukali, wansembe ndi mneneri adzandima ndi chakumwa chaukali, iwo amezedwa ndi vinyo, nasochera ndi chakumwa chaukali, adzandima popenya, naphunthwa poweruza.


Ansembe sanati, Ali kuti Yehova? Ndi iwo amene agwira malamulo sandidziwa Ine; ndi abusa omwe anandilakwira Ine, ndi aneneri ananenera mwa Baala, natsata zinthu zosapindula.


Sindinatuma aneneri awa, koma anathamanga; sindinanene ndi iwo, koma ananenera.


aneneri anenera monyenga nathandiza ansembe pakulamulira kwao; ndipo anthu anga akonda zotere; ndipo mudzachita chiyani pomalizira pake?


Pakuti kuyambira wamng'ono kufikira wamkulu onse akhala akusirira; ndiponso kuyambira mneneri kufikira wansembe onse achita monyenga.


Usatulukire kumunda, usayenda m'njira; pakuti lupanga la amaliwongo ndi mantha ali m'mbali zonse.


Chifukwa chake ndidzapereka akazi ao kwa ena, ndi minda yao kwa iwo adzalowamo; pakuti onse kuyambira wamng'ono kufikira wamkulu asirirasirira; kuyambira mneneri kufikira wansembe onse achita zonyenga.


Onani, Yehova; pakuti ndavutika, m'kati mwanga mugwedezeka; mtima wanga wasanduka mwa ine; pakuti ndapikisana nanu ndithu; kunjako lupanga limangopha ana; m'nyumba muli imfa.


Tauka, tafuula usiku, poyamba kulonda; tsanulira mtima wako ngati madzi pamaso pa Ambuye; takwezera maso ako kwa Iye, chifukwa cha moyo wa tiana tako, timene tilefuka ndi njala pa malekezero a makwalala onse.


Ophedwa ndi lupanga amva bwino kupambana ophedwa ndi njala; pakuti amenewa angokwalika napyozedwa, posowa zipatso za m'munda.


Kunja kuli lupanga, ndi m'katimo muli mliri ndi njala; wokhala kuthengo adzafa ndi lupanga, ndi wokhala m'mzindawo njala ndi mliri zidzamutha.


Ndipo Ine ndakupatsaninso mano oyera m'mizinda yanu yonse, ndi kusowa mkate m'malo mwanu monse; koma simunabwerere kudza kwa Ine, ati Yehova.


Akulu ake aweruza chifukwa cha mphotho, ndi ansembe ake aphunzitsa chifukwa cha malipo, ndi aneneri ake alosa chifukwa cha ndalama; koma atsamira pa Yehova, nati, Kodi Yehova sali pakati pa ife? Palibe choipa chodzatigwera.


Yehova adzamukitsa inu, ndi mfumu yanu imene mudzadziikira, kwa mtundu wa anthu umene simuudziwa, inu kapena makolo anu; ndipo mudzatumikirako milungu ina ya mitengo ndi miyala.


Ndipo Yehova adzakubalalitsani mwa mitundu yonse ya anthu, kuyambira malekezero a dziko lapansi kufikira malekezero a dziko lapansi; ndipo kumeneko mudzatumikira milungu ina, imene simunaidziwe, inu ndi makolo anu, yamitengo ndi yamiyala.


Ndipo m'chisiriro adzakuyesani malonda ndi mau onyenga; amene chiweruzo chao sichinachedwe ndi kale lomwe, ndipo chitayiko chao sichiodzera.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa