Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 13:22 - Buku Lopatulika

22 Ndipo ngati udzati m'mtima mwako, Zimenezi zandifikira ine chifukwa ninji? Chifukwa cha choipa chako chachikulu nsalu zako zoyesa mfula zasanduka mbudulira, ndi zitendene zako zaphwetekwa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 Ndipo ngati udzati m'mtima mwako, Zimenezi zandifikira ine chifukwa ninji? Chifukwa cha choipa chako chachikulu nsalu zako zoyesa mfula zasanduka mbudulira, ndi zithende zako zaphwetekwa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 Mukamadzifunsa kuti, ‘Kodi zimenezi zatigwera bwanji?’ Nchifukwa cha machimo anu ambiri kuti zovala zanu zikwinzidwe, ndipo kuti akuchiteni zankhanza.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 Ndipo ngati udzadzifunsa kuti, “Kodi zimenezi zandichitikira chifukwa chiyani?” Ndi chifukwa cha machimo anu ambiri kuti zovala zanu zingʼambike ndiponso kuti akuchitireni nkhanza.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 13:22
24 Mawu Ofanana  

momwemo mfumu ya Asiriya idzatsogolera kwina am'nsinga a Ejipito, ndi opirikitsidwa a Etiopiya, ana ndi okalamba, amaliseche ndi opanda nsapato, ndi matako osavala, kuti achititse manyazi Ejipito.


chifukwa chake Ambuye adzachita nkanambo pa liwombo la ana aakazi a Ziyoni, ndipo Yehova adzavundukula m'chuuno mwao.


Chifukwa chake tsono, imva ichi, iwe wotsata zokondweretsa, amene umakhala mosatekeseka, amene umati mumtima mwako, Ine ndine, ndipo popanda ine palibenso wina; sindidzakhala monga mkazi wamasiye, kapena kudziwa kumwalira kwa ana;


Chifukwa chake Ine ndidzaonetsa zotopola mikawo zako, pamaso pako, ndipo manyazi ako adzaoneka.


Ndipo anthu amene adzanenera kwa inu adzaponyedwa kunja m'miseu ya Yerusalemu chifukwa cha chilala ndi lupanga; ndipo adzasowa akuwaika, ndi akazi ao, ndi ana ao aamuna ndi aakazi; ndipo ndidzatsanulira pa iwo zoipa zao.


Ndipo padzakhala pamene mudzati, Chifukwa chanji Yehova Mulungu wathu atichitira ife zonse izi? Ndipo udzayankha kwa iwo, Monga ngati mwandisiya Ine, ndi kutumikira milungu yachilendo m'dziko lanu, momwemo mudzatumikira alendo m'dziko silili lanu.


Yerusalemu wachimwa kwambiri; chifukwa chake wasanduka chinthu chonyansa; onse akuulemekeza aupeputsa, pakuti auona wamaliseche; inde, uusa moyo, nubwerera m'mbuyo.


Adzakuvulanso zovala zako, ndi kukuchotsera zokometsera zako zokongola.


Ndipo Efuremu anati, Zedi ndasanduka wolemera, ndadzionera chuma m'ntchito zonse ndinazigwira; sadzapeza mwa ine mphulupulu yokhala tchimo.


Ndipo tsopano ndidzaonetsa manyazi ake pamaso pa omkonda, popandanso wakumlanditsa m'dzanja langa.


ndingamvule wamaliseche, ndi kumuika ngati tsiku lija anabadwalo, ndi kumsanduliza ngati chipululu, ndi kumuika ngati dziko louma, ndi kumupha nalo ludzu;


Pakuti mai wao anachita chigololo; iye amene anali ndi pakati pa iwo anachita chamanyazi; pakuti anati, Ndidzatsata ondikondawo, akundipatsa ine chakudya changa, ndi madzi anga, ubweya wanga, ndi thonje langa, mafuta anga, ndi chakumwa changa.


Taona, nditsutsana nawe, ati Yehova wa makamu, ndidzaphimba nkhope yako ndi nsalu yako yoyesa mthendene; ndipo ndidzaonetsa amitundu umaliseche wako, ndi mafumu manyazi ako.


Ndipo kudzachitika nthawi yomweyi kuti ndidzasanthula Yerusalemu ndi nyali, ndipo ndidzalanga amunawo okhala ndi nsenga, onena m'mtima mwao, Yehova sachita chokoma, kapena kuchita choipa.


Ndipo mukati m'mtima mwanu, Tidzazindikira bwanji mau amene Yehova sananene?


Mukadzanena m'mtima mwanu, Amitundu awa andichulukira; ndikhoza bwanji kuwapirikitsa?


ndipo munganene m'mtima mwanu, Mphamvu yanga ndi mkono wanga wolimba zinandifunira chuma ichi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa