Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 13:20 - Buku Lopatulika

20 Tukulani maso anu, taonani iwo amene achokera kumpoto; zili kuti zoweta zinapatsidwa kwa iwe, zoweta zako zokoma?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

20 Tukulani maso anu, taonani iwo amene achokera kumpoto; zili kuti zoweta zinapatsidwa kwa iwe, zoweta zako zokoma?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

20 “Ŵeramukani, inu a ku Yerusalemu, muwone adani amene akuchokera kumpoto. Kodi nkhosa zimene adakusungitsani zili kuti, nkhosa zanu zokongola zija?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

20 Tukula maso ako kuti uwone amene akubwera kuchokera kumpoto. Kodi nkhosa zimene anakusungitsa zili kuti, nkhosa zanu zokongola zija?

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 13:20
14 Mawu Ofanana  

Mu unyinji wa anthu muli ulemu wa mfumu; koma popanda anthu kalonga aonongeka.


Ndipo Yehova anati kwa ine, Kuchokera kumpoto choipa chidzatulukira onse okhala m'dziko.


Pakuti taona, ndidzaitana mabanja onse a maufumu a kumpoto, ati Yehova; ndipo adzafika nadzaika yense mpando wachifumu wake pa zipata za Yerusalemu, ndi pa malinga onse ozinga pamenepo, ndi pa mizinda yonse ya Yuda.


Mbiri yamveka, taonani ikudza, ndi phokoso lalikulu lituluka m'dziko la kumpoto, likachititse mizinda ya Yuda bwinja, ndi mbuto ya nkhandwe.


Koma ngati simudzamva, moyo wanga udzalira m'tseri chifukwa cha kunyada kwanu; diso langa lidzalira kwambiri, lidzagwa misozi, chifukwa zoweta za Yehova zagwidwa m'nsinga.


Chifukwa chake atero Yehova, Mulungu wa Israele, ponenera abusa amene adyetsa anthu anga: Mwabalalitsa zoweta zanga, ndi kuzipirikitsa, ndipo simunazizonde; taonani, ndidzakusenzani inu kuipa kwa ntchito zanu, ati Yehova.


Ndipo makola amtendere adzaonongeka chifukwa cha mkwiyo woopsa wa Yehova.


Yehova atero, Taona, mtundu wa anthu uchokera kumpoto; ndi mtundu waukulu udzaukitsidwa ku malekezero a dziko lapansi.


Pakuti taonani, ndiukitsa Ababiloni, mtundu uja wowawa ndi waliwiro, wopitira pa chitando cha dziko lapansi, kulowa m'malo mosati mwao, mukhale mwaomwao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa