Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 13:16 - Buku Lopatulika

16 Lemekezani Yehova Mulungu wanu, kusanade, mapazi anu asanaphunthwe pa mapiri achizirezire; nimusanayembekeze kuunika, Iye asanasandutse kuunikaku mthunzi wa imfa, ndi kukuyesa mdima wa bii.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Lemekezani Yehova Mulungu wanu, kusanade, mapazi anu asanakhumudwe pa mapiri achizirezire; nimusanayembekeze kuunika, Iye asanasandutse kuunikaku mthunzi wa imfa, ndi kukuyesa mdima wa bii.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Mlemekezeni Chauta, Mulungu wanu, asanagwetse mdima, mapazi anu asanakhumudwe m'chisisira cham'mapiri, asanasandutse kuŵala, kumene mukukufuna, kuti kukhale mdima wandiweyani.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Lemekezani Yehova Mulungu wanu asanagwetse mdima, mapazi anu asanayambe kupunthwa mʼchisisira chamʼmapiri. Asanasandutse kuwala mukuyembekezerako kukhala mdima wandiweyani.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 13:16
36 Mawu Ofanana  

Mdima ndi mthunzi wa imfa ziliyese laolao; mtambo ulikhalire; zonse zodetsa usana bii ziliopse.


Iwo akukhala mumdima ndi mu mthunzi wa imfa, omangika ndi kuzunzika ndi chitsulo;


Anawatulutsa mumdima ndi mu mthunzi wa imfa, nadula zomangira zao.


Perekani kwa Yehova ulemerero wa dzina lake, gwadirani Yehova moyera ndi mokometsetsa.


mungakhale munatithyola mokhala zilombo, ndi kutiphimba nao mthunzi wa imfa.


Ndipo Yehova anati kwa Mose, Tambasulira dzanja lako kuthambo, ndipo padzakhala mdima padziko la Ejipito, ndiwo mdima wokhudzika.


Njira ya oipa ikunga mdima; sadziwa chimene chiwaphunthwitsa.


Inde, munthu akakhala ndi moyo zaka zambiri, akondwere ndi zonsezo; koma akumbukire masiku amdima kuti adzachuluka. Zonse zilinkudza zili zachabe.


Ndipo iwo adzawabangulira tsiku limenelo ngati kukokoma kwa nyanja; ndipo wina ayang'ana padziko, taonani mdima ndi nsautso, kuyera kwadetsedwanso m'mitambo yake.


Tiyambasira khoma ngati wakhungu, inde tiyambasa monga iwo opanda maso; tiphunthwa usana monga m'chizirezire; tili m'malo amdima ngati akufa.


Chifukwa chake chiweruziro chili patali ndi ife, ndi chilungamo sichitipeza; tiyang'anira kuunika, koma taona mdima; tiyang'anira kuyera, koma tiyenda mu usiku.


Pakuti taona, mdima udzaphimba dziko lapansi, ndi mdima wa bii mitundu ya anthu; koma Yehova adzakutulukira ndi ulemerero wake udzaoneka pa iwe.


nadzayang'ana padziko, koma taonani, nkhawa ndi mdima, kuziya kwa nsautso; ndi mdima woti bii udzaingitsidwa.


Kodi mwakanadi Yuda? Kodi mtima wanu wanyansidwa ndi Ziyoni? Bwanji mwatipanda ife, ndipo tilibe kuchira? Tinayembekeza mtendere, koma sizinafike zabwino; tinayembekeza nthawi yakuchira, ndipo taonani mantha!


Osati Ali kuti Yehova amene anatikweza kuchokera kudziko la Ejipito, natitsogolera m'chipululu, m'dziko loti see ndi la maenje, m'dziko la chilala ndi la mthunzi wa imfa, m'dziko losapitanso anthu, losamangamo anthu?


Chifukwa chake njira yao idzakhala kwa iwo yonga malo akuterereka m'mdima; adzachotsedwa, nadzagwa momwemo; pakuti ndidzawatengera zoipa, chaka cha kulangidwa kwao, ati Yehova.


Ndinaona dziko lapansi, ndipo taona, linali lopasuka lopanda kanthu; ndipo ndinaona kumwamba, kunalibe kuunika.


Anthu anga anakhala nkhosa zotayika; abusa ao anazisokeretsa pa mapiri onyenga; achoka kuphiri kunka kuchitunda; aiwala malo ao akupuma.


Chifukwa chake atero Yehova, Taona, ndidzaikira anthuwa zophunthwitsa; ndipo atate ndi ana adzakhumudwa nazo pamodzi; munthu ndi mnzake adzatayika.


Tinayang'anira mtendere, koma panalibe zabwino; ndi nthawi ya moyo, ndipo taona kuopsedwa!


Maso athu athedwa, tikali ndi moyo, poyembekeza thandizo chabe; kudikira tinadikira mtundu wosatha kupulumutsa.


Ndalozetsa nsonga ya lupanga kuzipata zao zonse, kuti mtima wao usungunuke, ndi kukhumudwa kwao kuchuluke; ha! Analituula linyezimire, analisongoza liphe.


Monga mbusa afunafuna nkhosa zake tsiku lokhala iye pakati pa nkhosa zake zobalalika, momwemo ndidzafunafuna nkhosa zanga; ndipo ndidzawalanditsa m'malo monse anabalalikamo tsiku la mitambo ndi la mdima.


Ndipo sindidzakumvetsanso za manyazi a amitundu, ndipo sudzasenzanso mtonzo wa mitundu ya anthu, kapena kukhumudwitsanso anthu ako, ati Ambuye Yehova.


tsiku la mdima, la mdima wandiweyani, tsiku la mitambo, mitambo yochindikira, ngati m'mbandakucha moyalika pamapiri; mtundu waukulu ndi wamphamvu, panalibe wotere ndi kale lonse, sipadzakhalanso wotere utapita uwu, kufikira zaka za mibadwo yambiri.


Pakuti taona, Iye amene aumba mapiri, nalenga mphepo, nafotokozera munthu maganizo ake, nasanduliza m'mawa ukhale mdima, naponda pa misanje ya dziko lapansi, dzina lake ndiye Yehova Mulungu wa makamu.


Tsoka inu akufuna tsiku la Yehova? Mudzapindulanji nalo tsiku la Yehova? Ndilo mdima, si kuunika ai.


Mukapanda kumvera, mukapanda kuliika mumtima mwanu, kupatsa dzina langa ulemerero, ati Yehova wa makamu, ndidzakutumizirani temberero, ndi kutemberera madalitso anu; inde, ndawatemberera kale chifukwa simuliika mumtima.


Pamenepo Yesu anati kwa iwo, Katsala kanthawi kakang'ono ndipo kuunika kuli mwa inu. Yendani pokhala muli nako kuunika, kuti mdima sungakupezeni; ndipo woyenda mumdima sadziwa kumene amukako.


Ndipo Yoswa anati kwa Akani, Mwana wanga, uchitiretu ulemu Yehova Mulungu wa Israele, numlemekeze Iye; nundiuze tsopano, wachitanji? Usandibisire.


Ndipo, Mwala wakukhumudwa nao, ndi thanthwe lophunthwitsa. Kwa iwo akukhumudwa ndi mau, pokhala osamvera, kumenekonso adaikidwako.


Chifukwa chake muzipanga zifanizo za mafundo anu, ndi zifanizo za mbewa zanu zimene ziipitsa dziko; ndipo muchitire ulemu Mulungu wa Israele; kuti kapena adzaleza dzanja lake pa inu, ndi pa milungu yanu, ndi padziko lanu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa