Yeremiya 13:13 - Buku Lopatulika13 Ndipo udzati kwa iwo, Atero Yehova, Taonani, ndidzadzaza ndi chiledzero onse okhala m'dziko muno, ngakhale mafumu onse amene akhala pa mpando wachifumu wa Davide, ndi ansembe, ndi aneneri, ndi onse okhala mu Yerusalemu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201413 Ndipo udzati kwa iwo, Atero Yehova, Taonani, ndidzadzaza ndi chiledzero onse okhala m'dziko muno, ngakhale mafumu onse amene akhala pa mpando wachifumu wa Davide, ndi ansembe, ndi aneneri, ndi onse okhala m'Yerusalemu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa13 Tsono ukaŵauze kuti, Chauta akuti, Ndidzaŵamwetsa vinyo anthu onse am'dzikomo mpaka kuledzera. Anthuwo ndi aŵa: mafumu okhala pa mpando wa Davide, ansembe, aneneri, ndi onse okhala mu Yerusalemu. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero13 Tsono iwe uwawuze kuti, Yehova akuti ‘Ine ndidzaledzeretsa anthu onse okhala mʼdziko muno, kuyambira mafumu amene amakhala pa mpando waufumu wa Davide, ansembe, aneneri, pamodzi ndi anthu onse amene akukhala mu Yerusalemu. Onani mutuwo |