Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 12:9 - Buku Lopatulika

9 Cholowa changa chili kwa ine ngati mbalame yamawalamawala yolusa? Kodi mbalame zolusa zimzinga ndi kudana naye? Mukani, musonkhanitse zilombo za m'thengo, mudze nazo zidye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Cholowa changa chili kwa ine ngati mbalame yamawalamawala yolusa? Kodi mbalame zolusa zimzinga ndi kudana naye? Mukani, musonkhanitse zilombo za m'thengo, mudze nazo zidye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Anthu anga osankhidwa ali ngati mbalame yamaŵangamaŵanga imene akabaŵi aizinga kuchokera konsekonse. Kasonkhanitseni nyama zakuthengo, mubwere nazo ku phwando.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Anthu anga amene ndinawasankha asanduka ngati mbalame yolusa yamawangamawanga imene akabawi ayizinga. Pitani, kasonkhanitseni nyama zakuthengo. Mubwere nazo kuti zidzadye mbalameyo.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 12:9
15 Mawu Ofanana  

Ndipo Yehova anamtumizira magulu a Ababiloni, ndi magulu a Aaramu, ndi magulu a Amowabu, ndi magulu a ana a Amoni, nawatumiza pa Yuda kuliononga, monga mwa mau a Yehova adawanena ndi dzanja la atumiki ake aneneriwo.


Maso a munthu akuyang'anira kumwamba adzatsitsidwa, ndi kudzikweza kwa anthu kudzaweramitsidwa pansi; ndipo Yehova yekha adzakwezedwa tsiku limenelo.


Chifukwa padzakhala tsiku la Yehova wa makamu pa zonse zonyada ndi zakudzikuza, ndi pa zonse zotukulidwa; ndipo zidzatsitsidwa;


Inu zilombo zonse za m'thengo, idzani kulusa, inde zilombo inu nonse za m'nkhalango.


Ndipo ndidzaika pa iwo mitundu inai, ati Yehova, lupanga lakupha, agalu akung'amba, mbalame za m'mlengalenga, ndi zilombo zapansi, zakulusa ndi kuononga.


Ana a mikango anambangulira iye, nakweza mau; anapasula dziko lake, mizinda yake yatenthedwa, mulibenso wokhalamo.


ndidzapereka iwo m'dzanja la adani ao, ndi m'dzanja la iwo akufuna moyo wao; ndipo mitembo yao idzakhala chakudya cha mbalame za mlengalenga, ndi cha zilombo za padziko lapansi.


Ndipo mitembo ya anthu awa idzakhala zakudya za mbalame za mlengalenga, ndi za zilombo za dziko lapansi; palibe amene adzaziopsa.


Ziyoni atambasula manja ake, palibe wakumtonthoza; Yehova walamulira kuti omzungulira Yakobo akhale adani ake; Yerusalemu wasanduka chinthu chonyansa pakati pao.


M'mwemo zinamwazika posowa mbusa, ndipo zinakhala chakudya cha zilombo zilizonse zakuthengo, popeza zinamwazika.


Ndipo nyanga khumi udaziona, ndi chilombo, izi zidzadana ndi mkazi wachigololoyo, ndipo zidzamkhalitsa wabwinja wausiwa, ndi kudya nyama yake, ndipo zidzampsereza ndi moto.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa