Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 12:5 - Buku Lopatulika

5 Ngati wathamanga pamodzi ndi oyenda pansi, ndipo iwo anakulemetsa iwe, udzayesana nao akavalo bwanji? Ndipo ngakhale ukhazikika m'dziko lamtendere, udzachita chiyani m'kudzikuza kwa Yordani?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Ngati wathamanga pamodzi ndi oyenda pansi, ndipo iwo anakulemetsa iwe, udzayesana nao akavalo bwanji? Ndipo ngakhale ukhazikika m'dziko lamtendere, udzachita chiyani m'kudzikuza kwa Yordani?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Chauta adayankha kuti, “Ngati kukutopetsa kuthamanga ndi anthu, nanga udzapikisana bwanji ndi akavalo? Ngati mtima wako ulefuka m'dziko lokoma, nanga udzatani m'nkhalango ya ku Yordani?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Yehova anayankha kuti, “Ngati kukutopetsa kuthamanga pamodzi ndi anthu nanga ungapikisane bwanji ndi akavalo? Ngati ukupunthwa ndi kugwa pa malo abwino, udzatha bwanji kuthamanga mʼnkhalango za ku Yorodani?

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 12:5
14 Mawu Ofanana  

Awa ndi omwe aja anaoloka Yordani mwezi woyamba, atadzala kusefukira magombe ake onse; nathawitsa onse okhala m'zigwa kum'mawa ndi kumadzulo.


Madzi akuya aitanizana ndi madzi akuya, pa mkokomo wa matiti anu; mafunde onse a nyondonyondo anandimiza ine.


Ukalefuka tsiku la tsoka mphamvu yako ichepa.


Mwananga, usapeputse mwambo wa Yehova, ngakhale kutopa ndi kudzudzula kwake;


Chifukwa chake atero Yehova za anthu a Anatoti, amene afuna moyo wanga, kuti, Usanenere m'dzina la Yehova, ungafe ndi mkono wathu;


Ndipo panali, pamene Yeremiya anatha kunena mau onse amene Yehova anamuuza iye kuti anene kwa anthu onse, ansembe ndi aneneri ndi anthu onse anamgwira iye, ndi kuti, Udzafa ndithu.


Ndipo mfumu inauza Yerameele mwana wake wa mfumu, ndi Seraya mwana wa Aziriele, ndi Selemiya mwana wa Abideele, kuti awagwire Baruki mlembi ndi Yeremiya mneneri; koma Yehova anawabisa.


Taona, wina adzakwerera mudzi wolimba ngati mkango wochokera ku Yordani wosefuka; koma dzidzidzi ndidzamthamangitsa amchokere; ndipo aliyense amene asankhidwa, ndidzamuika woyang'anira wake, pakuti wakunga Ine ndani? Adzandiikira nthawi ndani? Ndipo mbusa adzaima pamaso panga ndani?


Taonani, mtundu uja adzakwerera mudzi wolimba ngati mkango wochokera ku Yordani wosefuka; koma dzidzidzi ndidzauthamangitsa umchokere, ndipo aliyense amene asankhidwa, ndidzamuika woyang'anira wake; pakuti wakunga Ine ndani? Adzandiikira nthawi ndani? Ndipo mbusa adzaima pamaso panga ndani?


Ndipo pamene iwo akusenza likasa anafika ku Yordani, nathibika m'mphepete mwa madzi mapazi a ansembe akusenza likasa, pakuti Yordani asefuka m'magombe ake onse, nyengo yonse ya masika,


Okondedwa, musazizwe ndi mayesedwe amoto adakugwerani inu akhale chakukuyesani, ngati chinthu chachilendo chachitika nanu:


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa