Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 12:12 - Buku Lopatulika

12 Akufunkha afika pa mapiri oti see m'chipululu; pakuti lupanga la Yehova lilusa kuyambira pa mbali ina ya dziko kufikira kumbali ina; palibe thupi lokhala ndi mtendere.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Akufunkha afika pa mapiri oti see m'chipululu; pakuti lupanga la Yehova lilusa kuyambira pa mbali ina ya dziko kufikira kumbali ina; palibe thupi lokhala ndi mtendere.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Anthu oononga abalalikira ku zitunda zonse zam'chipululu. Ndipo Ine Chauta ndatuma ankhondo kuti akanthe dziko lonse, kuyambira ku malire ena mpaka ku malire enanso. Palibe aliyense amene angapeze mtendere.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Anthu onse owononga abalalikira ku zitunda zonse za mʼchipululu. Yehova watuma ankhondo ake kudzawatha kuyambira kumalire ena a dziko mpaka ku malire enanso a dziko, ndipo palibe amene adzakhale pa mtendere.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 12:12
31 Mawu Ofanana  

Lupanga la Yehova lakhuta ndi mwazi, lanona ndi mafuta ndi mwazi wa anaankhosa, ndi mbuzi, ndi mafuta a impso ya nkhosa zamphongo; pakuti Yehova ali ndi nsembe mu Bozira, ndi ophedwa ambiri m'dziko la Edomu.


Palibe mtendere, ati Mulungu wanga, kwa oipa.


Ndipo padzakhala, pamene adzati kwa iwe, Titulukire kuti? Pamenepo uziti, Atero Yehova: Amene a kuimfa, anke kuimfa; amene a kulupanga, anke kulupanga; amene a kunjala, anke kunjala; ndi amene a kunsinga, anke kunsinga.


Pakuti Yehova atero, Usalowe m'nyumba ya maliro, usanke kukachita maliro ao, kapena kuwalirira; pakuti ndachotsa mtendere wanga pa anthu awa, chifundo ndi nsoni zokoma, ati Yehova.


Ndipo dziko lonseli lidzakhala labwinja, ndi chizizwitso, ndipo mitundu iyi idzatumikira mfumu ya ku Babiloni zaka makumi asanu ndi awiri.


Kwezera maso ako kumapiri oti see, nuone: sanagone ndi iwe kuti? Panjira wakhalira iwo, monga Mwarabu m'chipululu; ndipo waipitsa dziko ndi zigololo zako, ndi zoipa zako.


Mau amveka pa mapiri oti see, kulira ndi kupempha kwa ana a Israele; pakuti anaipitsa njira yao, naiwala Yehova Mulungu wao.


Pakuti Yehova atero: Tamva ife mau akunthunthumira, ndi amantha, si amtendere.


Chifukwa chake Yehova atero: Simunandimvere Ine, kuti mulalikire ufulu, munthu yense kwa mbale wake, ndi munthu yense kwa mnzake; taonani, ndilalikira kwa inu ufulu, ati Yehova, wa kulupanga, kumliri, ndi kunjala; ndipo ndidzakuperekani mukhale oopsetsa m'maufumu onse a dziko lapansi.


Pakuti Yehova atero, Dziko lonse lidzakhala bwinja koma sindidzatsirizitsa.


Pakuti tsikulo ndi la Ambuye, Yehova wa makamu, tsiku lakubweza chilango, kuti abwezere chilango adani ake; ndipo lupanga lidzadya, lidzakhuta, nilidzamwetsa mwazi wao; pakuti Ambuye, Yehova wa makamu, ali ndi nsembe m'dziko la kumpoto pamtsinje wa Yufurate.


Iwe lupanga la Yehova, atsala masiku angati osakhala chete iwe? Dzilonge wekha m'chimake; puma, nukhale chete.


Palibenso kutamanda Mowabu; mu Hesiboni anamlingiririra zoipa, ndi kuti, Tiyeni, tiwathe asakhalenso mtundu wa anthu. Iwenso, Madimeni, udzatontholetsedwa, lupanga lidzakulondola iwe.


Tinayang'anira mtendere, koma panalibe zabwino; ndi nthawi ya moyo, ndipo taona kuopsedwa!


Watalikitsanso moyo wanga ndi mtendere; ndinaiwala zabwino.


Kapena ndikadza padziko ndi lupanga, ndi kuti, Lupanga lipite pakati padziko, kuti ndilidulire munthu ndi nyama;


Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, nenera, nuziti, Atero Ambuye Yehova za ana a Amoni, ndi za chitonzo chao; nuziti, Lupanga, lupanga lasololedwa, latuulidwa, kuti likaphe, kuti liononge, likhale lonyezimira.


Popeza ndidzakulikhira olungama ndi oipa, chifukwa chake lupanga langa lidzasololokera anthu onse, kuyambira kumwera kufikira kumpoto;


Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti,


Wobadwa ndi munthu iwe, nenera ndi kuti, Atero Ambuye, Nena, Lupanga, lupanga lanoledwa, latuulidwanso;


Limodzi la magawo ake atatu utenthe ndi moto pakati pa mzinda pakutha masiku a kuzingidwa mzinda, nutenge gawo lina ndi kukwapulakwapula ndi lupanga pozungulira pake, nuwaze kumphepo gawo lotsala; pakuti ndidzasolola lupanga lakuwatsata.


Ndipo ndidzabalalitsa inu mwa amitundu, ndi kusolola lupanga kukutsatani; ndi dziko lanu lidzakhala lopasuka, ndi mizinda yanu idzakhala bwinja.


Angakhale alowa ndende pamaso pa adani ao, kumeneko ndidzalamulira lupanga, ndipo lidzawapha; ndipo ndidzayang'anitsa maso anga kwa iwowa, kuwachitira choipa, si chokoma ai.


Inunso Akusi, mudzaphedwa ndi lupanga langa.


Mivi yanga ndiiledzeretsa nao mwazi, ndi lupanga langa lidzalusira nyama; ndi mwazi wa ophedwa ndi ogwidwa, ndi mutu wachitsitsi wa mdani.


Ndipo anatuluka kavalo wina, wofiira: ndipo anampatsa iye womkwera mphamvu yakuchotsa mtendere padziko ndi kuti aphane; ndipo anampatsa iye lupanga lalikulu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa