Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 12:11 - Buku Lopatulika

11 Apayesa bwinja; pandilirira ine, pokhala bwinja; dziko lonse lasanduka bwinja; chifukwa palibe munthu wosamalira.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Apayesa bwinja; pandilirira ine, pokhala bwinja; dziko lonse lasanduka bwinja; chifukwa palibe munthu wosamalira.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Ndithu adausandutsa chipululu, ukundilirira Ine uli wokhawokha. Dziko lonse lasanduka chipululu, ndipo palibe amene akusamalako.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Unawusandutsadi chipululu. Ukanali wokhawokha chomwecho ukundilirira Ine. Dziko lonse lasanduka chipululu chifukwa palibe wolisamalira.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 12:11
23 Mawu Ofanana  

Kunka kunyumba ya maliro kupambana kunka kunyumba ya madyerero; pakuti kujako ndi matsiriziro a anthu onse; ndipo omwe ali ndi moyo adzakumbukirapo.


Chifukwa chake anatsanulira pa iye mkwiyo wake waukali, ndi mphamvu za nkhondo; ndipo unamyatsira moto kuzungulira kwake, koma iye sanadziwe; ndipo unamtentha, koma iye sanachisunge m'mtima.


Wolungama atayika, ndipo palibe munthu wosamalirapo; ndipo anthu achifundo atengedwa, palibe wolingalira kuti wolungama achotsedwa pa choipa chilinkudza.


Mbiri yamveka, taonani ikudza, ndi phokoso lalikulu lituluka m'dziko la kumpoto, likachititse mizinda ya Yuda bwinja, ndi mbuto ya nkhandwe.


Tsanulirani ukali wanu pa amitundu osakudziwani Inu, ndi pa mabanja osaitana dzina lanu; pakuti anadya Yakobo, inde, anamudya namutha, napasula mokhalamo mwake.


Yuda alira, ndipo zipata zake zilefuka, zikhala pansi zovekedwa ndi zakuda; mfuu wa Yerusalemu wakwera.


Ndipo ndidzayesa mzindawu chodabwitsa, ndi chotsonyetsa; onse amene adzapitapo adzadabwa ndi kutsonya chifukwa cha zopanda pake zonse.


Pakuti dziko ladzala ndi achigololo; pakuti chifukwa cha temberero dziko lirira, mabusa a kuchipululu auma; kuyenda kwao kuli koipa, ndi mphamvu yao siili yabwino.


Ndipo dziko lonseli lidzakhala labwinja, ndi chizizwitso, ndipo mitundu iyi idzatumikira mfumu ya ku Babiloni zaka makumi asanu ndi awiri.


Alalikira chipasuko chilalikire; pakuti dziko lonse lafunkhidwa; mahema anga afunkhidwa dzidzidzi, ndi nsalu zanga zotchinga m'kamphindi.


Pakuti Yehova atero, Dziko lonse lidzakhala bwinja koma sindidzatsirizitsa.


Chifukwa chimenecho dziko lidzalira maliro, ndipo kumwamba kudzada; chifukwa ndanena, ndatsimikiza mtima, sindinatembenuka, sindidzabwerera pamenepo.


Ulangizidwe, Yerusalemu, ungakuchokere moyo wanga, ndingakuyese iwe bwinja, dziko losakhalamo anthu.


Chifukwa cha mapiri ndidzagwa misozi ndi kulira, chifukwa cha mabusa a chipululu ndidzachita maliro, chifukwa apserera, kuti anthu sangathe kupitirirapo; ndiponso anthu sangathe kumva mau a ng'ombe zao; mbalame za mlengalenga ndi nyama zathawa, zapita.


Ndipo ndidzayesa Yerusalemu miyulu, mbuto ya ankhandwe; ndipo ndidzayesa mizinda ya Yuda bwinja, lopanda wokhalamo.


Kodi sindidzawalanga chifukwa cha izi? Ati Yehova; kodi moyo wanga sudzabwezera chilango mtundu wotere?


M'munda mwaonongeka, nthaka ilira; pakuti tirigu waonongeka, vinyo watsopano wamwelera, mafuta akudza pang'onong'ono.


Inde, ndidzapasula dzikoli, ndipo adani anu akukhala m'mwemo adzadabwa nako.


Nena kwa anthu onse a m'dziko, ndi kwa ansembe, kuti, Muja mukasala ndi kulira mwezi wachisanu, ndi wachisanu ndi chitatu, zaka izi makumi asanu ndi awiri, kodi mukasalira Ine, Inedi?


Mukapanda kumvera, mukapanda kuliika mumtima mwanu, kupatsa dzina langa ulemerero, ati Yehova wa makamu, ndidzakutumizirani temberero, ndi kutemberera madalitso anu; inde, ndawatemberera kale chifukwa simuliika mumtima.


Pakuti tidziwa kuti cholengedwa chonse chibuula, ndi kugwidwa m'zowawa pamodzi kufikira tsopano.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa