Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 12:10 - Buku Lopatulika

10 Abusa ambiri aononga munda wanga wampesa, apondereza gawo langa, pondikondweretsa apayesa chipululu chopanda kanthu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Abusa ambiri aononga munda wanga wamphesa, apondereza gawo langa, pondikondweretsa apayesa chipululu chopanda kanthu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Abusa ambiri adaononga munda wanga wamphesa, adapondereza munda wanga. Munda wokoma uja adausandutsa chipululu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Abusa ambiri anawononga munda wanga wa mpesa, anapondereza munda wanga; munda wanga wabwino uja anawusandutsa chipululu.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 12:10
21 Mawu Ofanana  

Yehova adzalowa m'bwalo la milandu ndi okalamba a anthu ake, ndi akulu ake: Ndinu amene mwadya munda wampesa, zofunkha za waumphawi zili m'nyumba zanu;


Chifukwa chake ndidzaipitsa akulu a Kachisi, ndipo ndidzasanduliza Yakobo akhale temberero, ndi Israele akhale chitonzo.


Anthu anu opatulika anakhala nacho kanthawi kokha; adani athu apondereza Kachisi wanu wopatulika.


Tsoka abusa amene athetsa nabalalitsa nkhosa za busa langa! Ati Yehova.


Ndipo makola amtendere adzaonongeka chifukwa cha mkwiyo woopsa wa Yehova.


Wasiya ngaka yake, monga mkango; pakuti dziko lao lasanduka chizizwitso chifukwa cha ukali wa lupanga losautsa, ndi chifukwa cha mkwiyo wake waukali.


taonani, Ine, ndidzatuma ndi kutenga mabanja onse a kumpoto, ati Yehova, ndipo ndidzatuma kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, mtumiki wanga, ndipo ndidzatengera iwo padziko lino, ndi pa okhalamo ake onse, ndi pa mitundu iyi yozungulira, ndipo ndidzathetsa iwo ndithu, ndi kuwayesa iwo chizizwitso, ndi chotsonyetsa, ndi bwinja lamuyaya.


Koma Ine ndinati, Ndidzakuika iwe bwanji mwa ana, ndi kupatsa iwe dziko lokondweretsa, cholowa chabwino cha makamu a mitundu ya anthu? Ndipo ndinati mudzanditcha Ine, Atate wanga; osatembenuka kuleka kunditsata Ine.


Ndipo akulu onse a mfumu ya ku Babiloni analowa, nakhala m'chipata chapakati, Neregali-Sarezere, Samugiri-Nebo, Sarisekimu, mkulu wa adindo, Neregali-Sarezare mkulu wa alauli ndi akulu ena onse a mfumu ya ku Babiloni.


Abusa ndi nkhosa zao adzadza kwa iye; adzamanga mahema ao pomzinga iye; adzadya yense pokhala pake.


Chifukwa cha mapiri ndidzagwa misozi ndi kulira, chifukwa cha mabusa a chipululu ndidzachita maliro, chifukwa apserera, kuti anthu sangathe kupitirirapo; ndiponso anthu sangathe kumva mau a ng'ombe zao; mbalame za mlengalenga ndi nyama zathawa, zapita.


Wobadwa ndi munthu iwe, Nenera motsutsa abusa a Israele; nenera, nuti nao abusawo, Atero Ambuye Yehova, Tsoka abusa a Israele odzidyetsa okha; kodi abusa sayenera kudyetsa nkhosa?


M'mwemo zinamwazika posowa mbusa, ndipo zinakhala chakudya cha zilombo zilizonse zakuthengo, popeza zinamwazika.


Pamenepo ndinamva wina woyera alikunena; ndi wina woyera anati kwa iye uja wanenayo, Masomphenya a nsembe yopsereza yachikhalire, ndi cholakwa chakupululutsa cha kupereka malo opatulika ndi khamulo ziponderezedwe, adzakhala mpaka liti?


koma ndidzawabalalitsa ndi kamvulumvulu mwa amitundu onse amene sanawadziwe. Motero dziko linakhala bwinja, m'mbuyo mwao; palibe munthu wopitapo ndi kubwererako; pakuti adaika dziko lofunikalo labwinja.


Chifukwa chake tsimikizani mumtima mwanu, kuti usanafike mlandu musalingirire chimene mudzayankha.


Ndipo bwalo la kunja kwa Kachisi ulisiye padera, osaliyesa; pakuti adapatsa ilo kwa amitundu; ndipo mzinda wopatulika adzaupondereza miyezi makumi anai mphambu iwiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa