Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 11:23 - Buku Lopatulika

23 ndipo sadzakhala nao otsalira; pakuti ndidzatengera choipa pa anthu a ku Anatoti, chaka cha kulangidwa kwao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

23 ndipo sadzakhala nao otsalira; pakuti ndidzatengera choipa pa anthu a ku Anatoti, chaka cha kulangidwa kwao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

23 Sadzapulumuka ndi mmodzi yemwe, chifukwa ndidzaononga anthu a ku Anatoti, chikadzafika chaka chao cha chilango.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

23 Sipadzakhala otsala ndi mmodzi yemwe, chifukwa ndidzalanga anthu a ku Anatoti chikadzafika chaka chawo cha chilango.’ ”

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 11:23
15 Mawu Ofanana  

Koma ine ndinanga mwanawankhosa wofatsa wotengedwa kukaphedwa; ndipo sindinadziwe kuti anandichitira ine chiwembu, kuti, Tiononge mtengo ndi zipatso zake, timdule iye padziko la amoyo, kuti dzina lake lisakumbukikenso.


Chifukwa chake njira yao idzakhala kwa iwo yonga malo akuterereka m'mdima; adzachotsedwa, nadzagwa momwemo; pakuti ndidzawatengera zoipa, chaka cha kulangidwa kwao, ati Yehova.


Taonani, ndiwayang'anira kuwachitira zoipa, si zabwino; ndipo amuna onse a Yuda okhala m'dziko la Ejipito adzathedwa ndi lupanga ndi njala, mpaka kutha kwao.


Ndiponso olipidwa ake ali pakati pake onga ngati anaang'ombe a m'khola; pakuti iwonso abwerera, athawa pamodzi, sanaime; pakuti tsiku la tsoka lao linawafikira, ndi nthawi ya kuweruzidwa kwao.


Ndipo iye wakuthawa chifukwa cha mantha adzagwa m'dzenje; ndi iye amene atuluka m'dzenje adzagwidwa m'khwekhwe; pakuti ndidzatengera pa iye, pa Mowabu, chaka cha kulangidwa kwao, ati Yehova.


Sindidzawalanga kodi chifukwa cha zimenezi? Ati Yehova; kodi moyo wanga sudzabwezera chilango mtundu wotere?


Kodi sindidzawalanga chifukwa cha zimenezi? Ati Yehova; kodi moyo wanga sudzabwezera chilango mtundu woterewu?


Iphani ng'ombe zamphongo zake zonse; zitsikire kukaphedwa; tsoka iwo! Pakuti tsiku lao lafika, tsiku la kulanga kwao.


Yehova wa makamu atero, Adzakunkha otsalira a Israele monga mpesa; bweza dzanja lako monga wakutchera mphesa m'madengu ake.


Kodi anakhala ndi manyazi pamene anachita zonyansa? Iai, sanakhale ndi manyazi, sananyale; chifukwa chake adzagwa mwa iwo amene akugwa, nthawi ya kuyang'aniridwa kwao adzagwetsedwa, ati Yehova.


Masiku a kulanga afika, masiku a kubwezera afika; Israele adzadziwa; mneneri ali wopusa, munthu wamzimu ali wamisala, chifukwa cha kuchuluka mphulupulu yako, ndi popeza udani ndi waukulu.


Ndipo nyumba ya Yakobo idzakhala moto, ndi nyumba ya Yosefe lawi, ndi nyumba ya Esau ngati chiputu, ndipo adzawatentha pakati pao, ndi kuwapsereza; ndipo sadzakhalapo otsalira nyumba ya Esau; pakuti Yehova wanena.


Wokoma wa iwo akunga mitungwi; woongoka wao aipa koposa mpanda waminga; tsiku la alonda ako la kulangidwa kwako lafika, tsopano kwafika kuthedwa nzeru kwao.


ndipo adzakupasula iwe, ndi ana ako mwa iwe; ndipo sadzasiya mwa iwe mwala wina pamwala unzake; popeza sunazindikire nyengo ya mayang'aniridwe ako.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa