Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 11:22 - Buku Lopatulika

22 chifukwa chake atero Yehova wa makamu, Taonani, ndidzalanga iwo; anyamata adzafa ndi lupanga; ana ao aamuna ndi aakazi adzafa ndi njala;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 chifukwa chake atero Yehova wa makamu, Taonani, ndidzalanga iwo; anyamata adzafa ndi lupanga; ana ao aamuna ndi aakazi adzafa ndi njala;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 Nchifukwa chake Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Ndidzaŵalanga. Anyamata ao adzaphedwa ku nkhondo. Ana ao aamuna ndi aakazi adzafa ndi njala.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 koma Yehova Wamphamvuzonse akuti, ‘Ine ndidzawalanga. Achinyamata awo adzaphedwa ndi lupanga, ana awo aamuna ndi aakazi adzafa ndi njala.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 11:22
9 Mawu Ofanana  

Pakuti Iye anawakweretsera mfumu ya Ababiloni, ndiye anawaphera anyamata ao ndi lupanga, m'nyumba ya malo ao opatulika, osachitira chifundo mnyamata kapena namwali, mkulu kapena nkhalamba; Mulungu anawapereka onse m'dzanja lake.


Chifukwa chake mupereke ana ao kunjala, mupereke iwo kumphamvu ya lupanga; akazi ao akhale opanda ana, ndi amasiye; amuna ao aphedwe ndi imfa, ndi anyamata ao apandidwe ndi lupanga kunkhondo.


Ndipo ndidzakulangani inu monga mwa chipatso cha ntchito zanu, ati Yehova; ndipo ndidzayatsa moto m'nkhalango mwake, ndipo udzatha zonse zomzungulira iye.


Ndipo ndidzalanga iwo okhala m'dziko la Ejipito, monga ndinalanga Yerusalemu, ndi lupanga, ndi njala, ndi mliri;


Chifukwa chake anyamata ake adzagwa m'miseu yake, ndipo anthu onse a nkhondo adzatontholetsedwa tsiku lomwelo, ati Yehova wa makamu.


Pakuti imfa yakwera m'mazenera athu, yalowa m'nyumba mwathu; kuchotsa ana kubwalo, ndi anyamata kumiseu.


Wamng'ono ndi nkhalamba agona pansi m'makwalala; anamwali ndi anyamata anga agwa ndi lupanga; munawapha tsiku la mkwiyo wanu, munawagwaza osachitira chisoni.


Ndinatumiza mliri pakati panu monga mu Ejipito; anyamata anu ndawapha ndi lupanga, ndi kutenga akavalo anu; ndipo ndinakweretsa kununkha kwa chigono chanu kufikitsa kumphuno kwanu; koma simunabwerere kudza kwa Ine, ati Yehova.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa