Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 11:19 - Buku Lopatulika

19 Koma ine ndinanga mwanawankhosa wofatsa wotengedwa kukaphedwa; ndipo sindinadziwe kuti anandichitira ine chiwembu, kuti, Tiononge mtengo ndi zipatso zake, timdule iye padziko la amoyo, kuti dzina lake lisakumbukikenso.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

19 Koma ine ndinanga mwanawankhosa wofatsa wotengedwa kukaphedwa; ndipo sindinadziwa kuti anandichitira ine chiwembu, kuti, Tiononge mtengo ndi zipatso zake, timdule iye pa dziko la amoyo, kuti dzina lake lisakumbukikenso.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

19 Ndidakhala ngati mwanawankhosa amene akupita naye kokamupha. Sindidadziŵe kuti chidaloza pa ine chiwembu chimene ankakonzekera nkumanena kuti, “Tiyeni tiwudule mtengowu ukali moyo. Tiyeni timuphe munthu ameneyu, kuti asadzakumbukikenso.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

19 Ndinali ngati mwana wankhosa wofatsa amene akupita naye kukamupha; sindinkadziwa kuti chiwembu chimene ankakonzekeracho chinkaloza ine. Iwo amati: “Tiyeni timuphe munthu ameneyu kuti dzina lake lisadzakumbukiridwenso.”

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 11:19
28 Mawu Ofanana  

Munthu sadziwa mtengo wake; ndipo silipezeka m'dziko la amoyo.


Zidzukulu zake zidulidwe; dzina lao lifafanizidwe mu mbadwo ukudza.


Popeza sadzagwedezeka nthawi zonse; wolungama adzakumbukika ku nthawi yosatha.


Ndidzayenda pamaso pa Yehova m'dziko la amoyo.


Ndinafuulira kwa inu, Yehova; ndinati, Inu ndinu pothawirapo panga, gawo langa m'dziko la amoyo.


Ndikadapanda kukhulupirira kuti ndikaone ubwino wa Yehova m'dziko la amoyo, ndikadatani!


Pakuti ndamva ugogodi wa ambiri, mantha andizinga. Pondipangira chiwembu, anatsimikiza mtima kulanda moyo wanga.


Ndipo pakutsimphina ine anakondwera, nasonkhana pamodzi; akundipanda anandisonkhanira; ndipo sindinachidziwe, ananding'amba osaleka.


Potero Mulungu adzakupasula kunthawi zonse, adzakuchotsa nadzakukwatula m'hema mwako, nadzakuzula, kukuchotsa m'dziko la amoyo.


Amati, Tiyeni tiwaononge asakhalenso mtundu wa anthu; ndipo dzina la Israele lisakumbukikenso.


Amayesa wolungama wodala pomkumbukira; koma dzina la oipa lidzavunda.


Usabisalire, woipa iwe, pomanga wolungama; usapasule popuma iyepo.


Mnyamatayo amtsata posachedwa, monga ng'ombe ipita kukaphedwa; ndi monga unyolo umadza kulanga chitsiru;


Zipangizonso za womana zili zoipa; iye apangira ziwembu zakuononga waumphawi ndi mau onama, ngakhale pamene wosowa alankhula zoona.


Ndinati, Sindidzaona Yehova m'dziko la amoyo; sindidzaonanso munthu pamodzi ndi okhala kunja kuno;


Ndipo adzamenyana ndi iwe; koma sadzakuposa; chifukwa Ine ndili ndi iwe, ati Yehova, kukulanditsa.


Ndipo iwo anati, Tiyeni, tilingalire Yeremiya chomchitira choipa; pakuti chilamulo sichidzathera wansembe, kapena uphungu wanzeru, kapena mau mneneri. Tiyeni, timpande iye ndi lilime, tisamvere iye mau ake ali onse.


Pakuti ndamva kugogodera kwa ambiri, mantha pozungulira ponse. Neneza, ndipo tidzamneneza iye, ati atsamwali anga onse, amene ayang'anira kutsimphina kwanga; kapena adzakopedwa, ndipo ife tidzampambana iye, ndipo tidzambwezera chilango.


Ndipo panali, pamene Yeremiya anatha kunena mau onse amene Yehova anamuuza iye kuti anene kwa anthu onse, ansembe ndi aneneri ndi anthu onse anamgwira iye, ndi kuti, Udzafa ndithu.


Mwaona kubwezera kwao konse ndi zopangira zao zonse za pa ine.


Elamu ali komwe ndi gulu lake lonse lozinga manda ake; ophedwa onsewo, adagwa ndi lupanga; amene anatsikira osadulidwa kunsi kwake kwa dziko, amene anaopsetsa m'dziko la amoyo, nasenza manyazi ao, pamodzi ndi iwo akutsikira kudzenje.


Ndipo atapita masabata makumi asanu ndi limodzi mphambu awiri wodzozedwayo adzalikhidwa, nadzakhala wopanda kanthu; ndi anthu a kalonga wakudzayo adzaononga mzinda ndi malo opatulika; ndi kutsiriza kwake kudzakhala kwa chigumula, ndi kufikira chimaliziro kudzakhala nkhondo; chipasuko chalembedweratu.


Efuremu ndiye wozonda kwa Mulungu wanga; kunena za mneneri, msampha wa msodzi uli m'njira zake zonse, ndi udani m'nyumba ya Mulungu wake.


Wa Gadi, Eliyasafu mwana wa Deuwele.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa