Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 11:16 - Buku Lopatulika

16 Yehova anatcha dzina lako, Mtengo wa azitona wauwisi, wokoma wa zipatso zabwino; ndi mau a phokoso lalikulu wayatsa moto pamenepo, ndipo nthambi zake zathyoka.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Yehova anatcha dzina lako, Mtengo wa azitona wauwisi, wokoma wa zipatso zabwino; ndi mau a phokoso lalikulu wayatsa moto pamenepo, ndipo nthambi zake zathyoka.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Kale Chauta ankakuyerekezani ndi mtengo wa olivi wa masamba obiriŵira ndi wa zipatso zokongola. Koma tsopano adzautentha ndi mkuntho wamkokomo, ndipo nthambi zake zidzapserera.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Kale Yehova ankakutchani mtengo wa olivi wa masamba obiriwira, wokhala ndi zipatso zokongola. Koma tsopano adzawutentha ndi mkuntho wamkokomo ndipo nthambi zake zidzapserera.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 11:16
18 Mawu Ofanana  

Akhala wamuwisi pali dzuwa, ndi nthambi zake zitulukira pamunda pake.


Koma ine ndine ngati mtengo wauwisi wa azitona m'nyumba ya Mulungu. Ndikhulupirira chifundo cha Mulungu kunthawi za nthawi.


Unapserera ndi moto, unadulidwa; aonongeka pa kudzudzula kwa nkhope yanu.


Dzanja lanu likhale pa munthu wa padzanja lamanja lanu; pa mwana wa munthu amene munadzilimbikitsira.


Pakuti taonani, adani anu apokosera, ndipo okwiyira Inu aweramutsa mutu.


Ponyala nthambi zake zidzathyoledwa; akazi adzafika, nazitentha ndi moto, pakuti ali anthu opanda nzeru; chifukwa chake Iye amene anawalenga sadzawachitira chisoni, ndi Iye amene anawaumba sadzawakomera mtima.


Ndipo Ine ndinakuoka mpesa wangwiro, mbeu yoona; kodi bwanji wandisandukira Ine mbeu yopanda pake, ya mpesa wachilendo?


Ndipo ndidzakulangani inu monga mwa chipatso cha ntchito zanu, ati Yehova; ndipo ndidzayatsa moto m'nkhalango mwake, ndipo udzatha zonse zomzungulira iye.


Chifukwa chake, ati Ambuye Mulungu, Taonani, mkwiyo wanga ndi ukali wanga udzathiridwa pamalo ano, pa anthu, ndi pa nyama, ndi pa mitengo ya m'munda, ndi pa zipatso zapansi; ndipo udzatentha osazima.


Nthambi zake zidzatambalala, ndi kukoma kwake kudzanga kwa mtengo wa azitona, ndi fungo lake ngati Lebanoni.


Ndiponso tsopano lino nkhwangwa yaikidwa pa mizu ya mitengo: chifukwa chake mtengo uliwonse wosabala zipatso zabwino udulidwa nuponyedwa pamoto.


Ngati wina sakhala mwa Ine, watayika kunja monga nthambi, nafota; ndipo azisonkhanitsa nazitaya kumoto, nazitentha.


Mudzakhala nayo mitengo ya azitona m'malire anu onse, osadzola mafuta; popeza zipatso za mitengo ya azitona zidzapululuka.


Izo ndizo mitengo iwiri ya azitona ndi zoikaponyali ziwiri zakuima pamaso pa Ambuye wa dziko lapansi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa