Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 11:14 - Buku Lopatulika

14 Chifukwa chake usawapempherere anthu awa, usawakwezere iwo mfuu, kapena pemphero, pakuti sindidzamva iwo nthawi imene andifuulira Ine m'kusauka kwao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Chifukwa chake usawapempherere anthu awa, usawakwezere iwo mfuu, kapena pemphero, pakuti sindidzamva iwo nthawi imene andifuulira Ine m'kusauka kwao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Tsono iwe Yeremiya, usaŵapempherere anthu ameneŵa. Usaŵapepesere kwa Ine kapena kuŵadandaulira. Ndithu, Ine sindidzaŵamvera akadzandiitana pa nthaŵi ya mavuto ao.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 “Tsono iwe Yeremiya usawapempherere anthu amenewa ngakhale kuwadandaulira kapena kuwapepesera, chifukwa sindidzawamvera akadzandiyitana pa nthawi ya mavuto awo.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 11:14
12 Mawu Ofanana  

Ndikadasekera zopanda pake m'mtima mwanga, Ambuye sakadamvera.


ndipo tsopano ndileke, kuti ndipse mtima pa awo ndi kuwatha, ndi kukuza iwe ukhale mtundu waukulu.


Chifukwa chake atero Yehova, Taonani, ndidzatengera pa iwo choipa, chimene sangathe kuchipulumuka; ndipo adzandifuulira Ine, koma sindidzamvera iwo.


Ndipo Yehova anati kwa ine, Usapempherere anthu awa zabwino.


Pamene asala chakudya, sindidzamva kufuula kwao; ndipo pamene apereka nsembe yopsereza, ndi nsembe yaufa sindidzawalandira; koma ndidzawatha ndi lupanga, ndi chilala, ndi mliri.


Ndipo Yehova anati kwa ine, Ngakhale Mose ndi Samuele akadaima pamaso panga, koma mtima wanga sukadasamalira anthu awa; muwachotse iwo pamaso panga, atuluke.


Chifukwa chake iwe usapempherere anthu awa, usawakwezere iwo mfuu kapena pemphero, usandipembedze; pakuti Ine sindidzakumvera iwe.


Adzamuka ndi zoweta zao zazing'ono ndi zazikulu kufunafuna Yehova: koma sadzampeza; Iye wadzibweza kuwachokera.


Ndipo kunachitika, monga Iye anafuula, koma iwo sanamvere; momwemo iwo adzafuula, koma Ine sindidzamva, ati Yehova wa makamu;


Ndi ichi mubwereza kuchichita: mukuta guwa la nsembe la Yehova ndi misozi, ndi kulira, ndi kuusa moyo; momwemo Iye sasamaliranso chopereka, kapena kulandira mokondwera m'dzanja lanu.


Wina akaona mbale wake alikuchimwa tchimo losati la kuimfa, apemphere Mulungu, ndipo Iye adzampatsira moyo wa iwo akuchita machimo osati a kuimfa. Pali tchimo la kuimfa: za ililo sindinena kuti mupemphere.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa