Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 10:25 - Buku Lopatulika

25 Tsanulirani ukali wanu pa amitundu osakudziwani Inu, ndi pa mabanja osaitana dzina lanu; pakuti anadya Yakobo, inde, anamudya namutha, napasula mokhalamo mwake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

25 Tsanulirani ukali wanu pa amitundu osakudziwani Inu, ndi pa mabanja osaitana dzina lanu; pakuti anadya Yakobo, inde, anamudya namutha, napasula mokhalamo mwake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

25 Ukali wanu uyakire mitundu imene sikudziŵani, ndiye kuti anthu amene satama dzina lanu mopemba. Iwo adasakaza anthu anu ndi kuŵaononga kotheratu ndipo dziko lao adalisandutsa bwinja.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

25 Tsanulirani ukali wanu pa mitundu ya anthu amene sakudziwani, ndiye kuti mitundu ya anthu amene satama pa dzina lanu mopemba. Iwo aja anasakaza Yakobo; amusakaza kotheratu ndipo awononga dziko lake.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 10:25
28 Mawu Ofanana  

Zoonadi, zokhalamo osalungama zitero, ndi malo a iye amene sadziwa Mulungu ndi awa.


Kodi onse ochita zopanda pake sadziwa kanthu? Pakudya anthu anga monga akudya mkate, ndipo saitana pa Yehova.


Sanatero nao anthu a mtundu wina; ndipo za maweruzo ake, sanawadziwe. Aleluya.


Pondifika ine ochita zoipa kudzadya mnofu wanga, inde akundisautsa ndi adani anga, anakhumudwa iwo nagwa.


Muwatsanulire mkwiyo wanu, ndipo moto wa ukali wanu uwagwere.


Komabe iwe sunandiitane Ine, Yakobo; koma iwe walema ndi Ine, Israele.


Ndipo palibe amene aitana dzina lanu, amene adzikakamiza yekha kugwiritsa Inu; pakuti Inu mwatibisira nkhope yanu, ndipo mwatinyeketsa ndi zoipa zathu.


Aramu patsogolo ndi Afilisti pambuyo; ndipo iwo adzadya Israele ndi kukamwa koyasama. Mwa izi zonse mkwiyo wake sunachoke, koma dzanja lake lili chitambasulire.


Mau amene anadza kwa Yeremiya kuchokera kwa Yehova, kuti,


Chifukwa chake iwo akulusira iwe adzalusiridwanso; ndi adani ako onse, adzanka ku undende onsewo; ndipo iwo adzakufunkha iwe adzakhala chofunkha, ndipo onse akulanda iwe ndidzapereka kuti zilandidwe zao.


Israele ndiye nkhosa yolowerera, mikango yampirikitsa, poyamba inamudya mfumu ya Asiriya; ndipo pomaliza Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni wathyola mafupa ake.


Onse amene anazipeza anazidya; adani ao anati, Sitipalamula mlandu, chifukwa iwo anachimwira Yehova, ndiye mokhalamo zolungama, Yehova, chiyembekezo cha atate ao.


Kumina kwa akavalo ake kunamveka ku Dani; dziko lonse linanthunthumira pa kulira kwa akavalo akewo olimba; chifukwa afika, nadya dziko ndi zonse za momwemo; mzinda ndi amene akhalamo.


Mwaitana zondiopsa mozungulira ngati tsiku la msonkhano; panalibe wopulumuka ndi wotsala tsiku la mkwiyo wa Yehova; omwe ndinawaseweza ndi kuwalera, adaniwo anawatsiriza.


ndi iwo akubwerera osamtsata Yehova; ndi osamfuna Yehova, kapena kufunsira kwa Iye.


Chifukwa chake, mundilindire, ati Yehova, kufikira tsiku loukira Ine zofunkha; pakuti ndatsimikiza mtima Ine kusonkhanitsa amitundu, kuti ndimemeze maufumu kuwatsanulira kulunda kwanga, ndilo mkwiyo wanga wonse waukali; pakuti dziko lonse lapansi lidzathedwa ndi moto wa nsanje yanga.


Ndipo ndikwiya nao amitundu okhala osatekeseka ndi mkwiyo waukulu; pakuti ndinakwiya pang'ono, ndipo anathandizira choipa.


Atate wolungama, dziko lapansi silinadziwe Inu, koma Ine ndinadziwa Inu; ndipo iwo anazindikira kuti munandituma Ine;


Pakuti popita, ndi kuona zinthu zimene muzipembedza, ndipezanso guwa la nsembe lolembedwa potere, KWA MULUNGU WOSADZIWIKA. Chimene muchipembedza osachidziwa, chimenecho ndichilalikira kwa inu.


Ukani molungama, ndipo musachimwe; pakuti ena alibe chidziwitso cha Mulungu. Ndilankhula kunyaza inu.


kosati m'chisiriro cha chilakolako chonyansa, monganso amitundu osadziwa Mulungu;


m'lawi lamoto, ndi kubwezera chilango kwa iwo osamdziwa Mulungu, ndi iwo osamvera Uthenga Wabwino wa Ambuye wathu Yesu;


Ndipo ndinamva mau aakulu ochokera ku Kachisi, akunena kwa angelo asanu ndi awiri, Mukani, ndipo tsanulirani kudziko mbale zisanu ndi ziwiri za mkwiyo wa Mulungu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa