Yeremiya 10:23 - Buku Lopatulika23 Inu Yehova, ndidziwa kuti njira ya munthu sili mwa iye mwini; sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201423 Inu Yehova, ndidziwa kuti njira ya munthu sili mwa iye mwini; sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa23 Inu Chauta, ndikudziŵa kuti moyo umene ali nawo munthu si wake. Munthu sangathe kudzitsogolera yekha. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero23 Inu Yehova, ndikudziwa kuti moyo umene munthu ali nawo si wake; munthuyo sangathe kuwongolera mayendedwe ake. Onani mutuwo |
koma munadzikweza kutsutsana naye Ambuye wa Kumwamba; ndipo anabwera nazo zotengera za nyumba yake kwa inu; ndi inu ndi akulu anu, akazi anu ndi akazi anu aang'ono, mwamweramo vinyo; mwalemekezanso milungu yasiliva, ndi yagolide, yamkuwa, yachitsulo, yamtengo, ndi yamwala, imene siiona kapena kumva, kapena kudziwa; ndi Mulungu amene m'dzanja mwake muli mpweya wanu, ndi njira zanu zonse, yemweyo simunamchitire ulemu.