Yeremiya 10:22 - Buku Lopatulika22 Mbiri yamveka, taonani ikudza, ndi phokoso lalikulu lituluka m'dziko la kumpoto, likachititse mizinda ya Yuda bwinja, ndi mbuto ya nkhandwe. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201422 Mbiri yamveka, taonani ikudza, ndi phokoso lalikulu lituluka m'dziko la kumpoto, likachititse midzi ya Yuda bwinja, ndi mbuto ya nkhandwe. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa22 Tamvani, kukubwera mphekesera. Kumpoto kukuchokera chinamtindi chosokosa chodzasakaza mizinda ya Yuda, kuti isanduke bwinja, mokhala nkhandwe basi. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero22 Tamvani! kukubwera mphekesera, phokoso lalikulu la gulu la a ankhondo likumveka kuchokera kumpoto! Lidzasandutsa bwinja mizinda ya ku Yuda, malo okhala nkhandwe. Onani mutuwo |
taonani, Ine, ndidzatuma ndi kutenga mabanja onse a kumpoto, ati Yehova, ndipo ndidzatuma kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, mtumiki wanga, ndipo ndidzatengera iwo padziko lino, ndi pa okhalamo ake onse, ndi pa mitundu iyi yozungulira, ndipo ndidzathetsa iwo ndithu, ndi kuwayesa iwo chizizwitso, ndi chotsonyetsa, ndi bwinja lamuyaya.