Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 10:19 - Buku Lopatulika

19 Tsoka ine, ndalaswa! Bala langa lindipweteka; koma ine ndinati, Ndithu vuto langa ndi ili, ndipirire nalo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

19 Tsoka ine, ndalaswa! Bala langa lindipweteka; koma ine ndinati, Ndithu vuto langa ndi ili, ndipirire nalo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

19 Ali apa amvekere, “Kalanga ine chifukwa cha kupweteka koopsa! Bala langa ndi lomvetsa chisoni. Kale ndinkati chimenechi ndi chilango changa, ndingochipirira basi.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

19 Aliyense ankangoti, “Mayo ine, chifukwa cha kupweteka kwanga! Chilonda changa nʼchachikulu!” Koma ine ndinkaganiza kuti, “Ndithu, ili ndi vuto langa basi, choncho ndingolipirira.”

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 10:19
17 Mawu Ofanana  

Ndinakhala duu, sindinatsegule pakamwa panga; chifukwa inu mudachichita.


Ndipo ndinati, Chindiwawa ichi; koma ndikumbukira zaka za dzanja lamanja la Wam'mwambamwamba.


Ndipo ndidzalindira Yehova, amene wabisira a nyumba ya Yakobo nkhope yake, ndipo ndidzamyembekeza Iye.


Ndipo udzati kwa iwo mau awa, Maso anga agwe misozi usana ndi usiku, asaleke; pakuti namwali mwana wa anthu anga wasweka ndi kusweka kwakukulu, ndi bala lopweteka kwambiri.


Zingakhale zoipa zathu zititsutsa ife, chitani Inu chifukwa cha dzina lanu, Yehova; pakuti zobwerera zathu zachuluka; takuchimwirani Inu.


Inu Yehova, chiyembekezo cha Israele, onse amene akukusiyani Inu adzakhala ndi manyazi; onse ondichokera Ine adzalembedwa m'dothi, chifukwa asiya Yehova, kasupe wa madzi amoyo.


Matumbo anga, matumbo anga! Ndipoteka pamtima panga penipeni; mtima wanga sukhala pansi m'kati mwanga; sindithai kutonthola; pakuti wamva, moyo wanga, mau a lipenga, mbiri ya nkhondo.


Pakuti ndamva kubuula ngati kwa mkazi wobala, ndi msauko ngati wa mkazi wobala mwana wake woyamba, mau a mwana wamkazi wa Ziyoni wakupuma mosiyiza, wakutambasula manja ake, ndi kuti, Tsoka ine tsopano! Pakuti moyo wanga walefuka chifukwa cha ambanda.


Bala la mwana wamkazi wa anthu anga ndaphwetekwa nalo; ndada mtima; kudabwa kwandigwira.


Ha, mutu wanga ukadakhala madzi, ndi maso anga kasupe wa misozi, kuti usana ndi usiku ndilirire ophedwa a mwana wamkazi wa anthu anga!


Uliralira usiku; misozi yake ili pa masaya ake; mwa onse amene anaukonda mulibe mmodzi wakuutonthoza: Mabwenzi ake onse auchitira ziwembu, asanduka adani ake.


M'diso mwanga mutsika mitsinje ya madzi chifukwa cha mwana wamkazi wa anthu a mtundu wanga woonongedwa.


Ndidzasenza mkwiyo wa Yehova, chifukwa ndamchimwira, mpaka andinenera mlandu wanga, ndi kundiweruzira mlandu wanga; adzanditulutsira kwa kuunika, ndipo ndidzapenya chilungamo chake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa