Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 10:18 - Buku Lopatulika

18 Pakuti atero Yehova, Taonani, ndidzaponya kunja okhala m'dziko ili tsopanoli, ndi kuwasautsa, kuti azindikire.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 Pakuti atero Yehova, Taonani, ndidzaponya kunja okhala m'dziko ili tsopanoli, ndi kuwasautsa, kuti azindikire.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 Chauta akunena kuti, “Tsopano ndichotsa anthu onse a m'dziko lino. Ndidzaŵagwetsa m'mavuto, mpaka aŵamve ndithu.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 Pakuti Yehova akuti, “Tsopano Ine ndidzachotsa anthu onse amene akukhala mʼdziko lino; adzakhala pa mavuto mpaka adzamvetsa.”

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 10:18
11 Mawu Ofanana  

Taona Yehova adzakuponya iwe zolimba, monga mwamuna wamphamvu, inde adzakufumbata zolimba.


chifukwa chake ndidzakutulutsani inu m'dziko muno munke kudziko limene simunadziwa, kapena inu kapena makolo anu; pamenepo mudzatumikira milungu ina usana ndi usiku, kumene sindidzachitira inu chifundo.


Ndipo ndidzakutulutsa iwe, ndi mai wako wakubala iwe, kulowa m'dziko lina, limene sunabadwiremo; m'menemo udzafa.


Mkwiyo wa Yehova sudzabwerera, mpaka atachita, mpaka atatha maganizo a mtima wake; masiku otsiriza mudzachidziwa bwino.


Ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, sindinanene chabe kuti ndidzawachitira choipa ichi.


Ndipo ndidzatengera anthu zowapsinja, kuti adzayenda ngati anthu akhungu, popeza anachimwira Yehova; ndi mwazi wao udzatsanulidwa ngati fumbi, ndi nyama yao idzanga ndowe.


Koma mau anga ndi malemba anga, amene ndinalamulira atumiki anga aneneriwo, kodi sanawapeze makolo anu? Ndipo anabwera, nati, Monga umo Yehova wa makamu analingirira kutichitira ife, monga mwa njira zathu ndi monga mwa machitidwe athu, momwemo anatichitira.


Ndipo adzakuzingani m'midzi mwanu monse, kufikira adzagwa malinga anu aatali ndi olimba, amene munawakhulupirira, m'dziko lanu lonse; inde, adzakuzingani m'midzi mwanu monse, m'dziko lanu lonse limene Yehova Mulungu wanu akupatsani.


Ngakhale anauka anthu kukulondolani, ndi kufuna moyo wanu, koma moyo wa mbuye wanga udzamangika m'phukusi la amoyo lakukhala ndi Yehova Mulungu wanu; koma Iye adzaponya miyoyo ya adani anu kuwataya monga chotuluka m'choponyera mwala.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa