Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 10:11 - Buku Lopatulika

11 Muzitero nao, milungu imene sinalenge miyamba ndi dziko lapansi, iyo idzatha kudziko lapansi, ndi pansi pa miyambayo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Muzitero nao, milungu imene sinalenga miyamba ndi dziko lapansi, iyo idzatha kudziko lapansi, ndi pansi pa miyambayo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Anthuwo mukaŵauze kuti, “Milungu imene sidalenge dziko lakumwamba ndi dziko lapansi, idzaonongeka ponseponse, pa dziko lapansi ndi pansi pa thambo.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 “Awuze anthu awa kuti, ‘Milungu iyi, imene sinalenge dziko lakumwamba ndi dziko lapansi, idzawonongeka pa dziko lapansi ndi pansi pa thambo.’ ”

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 10:11
14 Mawu Ofanana  

Pakuti milungu yonse ya mitundu ya anthu ndiyo mafano, koma Yehova analenga zakumwamba.


Ndimo mafano adzapita psiti.


Ndidzaonetsa chilungamo chako ndi ntchito zako sudzapindula nazo.


Ndiwo chabe, ndiwo chiphamaso; pa nthawi ya kulangidwa kwao adzatha.


Ndidzayatsa moto m'nyumba za milungu ya Ejipito; ndipo adzazitentha, nadzaitenga ndende; ndipo adzadzifunda ndi dziko la Ejipito, monga mbusa avala chovala chake; nadzatuluka m'menemo ndi mtendere.


Ndipo adzathyola mizati ya zoimiritsa za Kachisi wa dzuwa, ali m'dziko la Ejipito; ndi nyumba za milungu ya Aejipito adzazitentha ndi moto.


Lalikirani mwa amitundu, falikitsani, kwezani mbendera; falikitsani, musabise; munene, Babiloni wagwidwa, Beli wachitidwa manyazi, Merodaki wathyokathyoka, zosema zake zachitidwa manyazi, mafano ake athyokathyoka.


Ngwachabe, chiphamaso; nthawi ya kulangidwa kwao adzatayika.


mudzawalondola mokwiya ndi kuwaononga pansi pa thambo la Yehova.


Atero Ambuye Yehova, Ndidzaononganso mafano, ndi kuleketsa milungu yopanda pake ku Nofu; ndipo sadzaonekanso kalonga wochokera ku Ejipito, ndipo ndidzaopsa dziko la Ejipito.


Yehova adzawakhalira woopsa; pakuti adzaondetsa milungu yonse ya padziko lapansi; ndipo adzamlambira Iye, yense pamalo pake, a m'zisumbu zonse za amitundu.


Ndipo kudzachitika tsiku lomwelo, ati Yehova wa makamu, ndidzaononga maina a mafano m'dziko; ndipo sadzakumbukikanso; ndipo ndidzachotsa m'dziko aneneri ndi mzimu wachidetso.


Ndipo anagwira chinjoka, njoka yakaleyo, ndiye mdierekezi ndi Satana, nammanga iye zaka chikwi,


Ndipo m'mawa mwake polawirira, taonani, Dagoni adagwa pansi, nagona chafufumimba patsogolo pa likasa la Yehova; ndipo mutu wake ndi zikhato zonse ziwiri za manja ake zinagona zoduka pachiundo; Dagoni anatsala thupi lokha.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa