Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 1:18 - Buku Lopatulika

18 Chifukwa, taona, ndakuyesa iwe lero mzinda walinga, mzati wachitsulo, makoma amkuwa, padziko lonse, ndi pa mafumu a Yuda, ndi pa akulu ake, ndi pa ansembe ake, ndi pa anthu a m'dziko.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 Chifukwa, taona, ndakuyesa iwe lero mudzi walinga, mzati wachitsulo, makoma amkuwa, pa dziko lonse, ndi pa mafumu a Yuda, ndi pa akulu ake, ndi pa ansembe ake, ndi pa anthu a m'dziko.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 Lero ine ndikukulimbitsa ngati mzinda wamalinga, mzati wachitsulo, ndiponso ngati makoma amkuŵa, kuti usachite mantha ndi wina aliyense m'dziko lonse, kaya ndi mafumu a ku Yuda, nduna zakumeneko, ansembe kapena anthu wamba.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 Taona, lero ndakupanga kukhala ngati mzinda wotetezedwa, ngati mzati wachitsulo ndiponso ngati makoma a mkuwa kuti usaopsedwe ndi munthu aliyense wa mʼdzikomo; kaya ndi mafumu a Yuda, akuluakulu ake, ansembe ake, kapena munthu wamba wa mʼdzikomo.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 1:18
21 Mawu Ofanana  

Pakuti Ambuye Yehova adzandithangata Ine; chifukwa chake sindinasokonezedwa; chifukwa chake ndakhazika nkhope yanga ngati mwala, ndipo ndidziwa kuti sindidzakhala ndi manyazi.


Koma iwe ukwinde m'chuuno mwako, nuuke, nunene kwa iwo zonse zimene ndikuuza iwe; usaope nkhope zao ndingakuopetse iwe pamaso pao.


Ndipo adzamenyana ndi iwe; koma sadzakuposa; chifukwa Ine ndili ndi iwe, ati Yehova, kukulanditsa.


Kalanga ine, amai, pakuti mwandibala ine munthu wandeu, munthu wakutetana nalo dziko lonse lapansi! Sindinakongoletsa paphindu, anthu sanandikongoletse paphindu; koma iwo onse anditemberera.


Ndidzakuyesa iwe linga lamkuwa la anthu awa; ndipo adzamenyana ndi iwe, koma iwo sadzakuposa iwe; pakuti Ine ndili ndi iwe kuti ndikupulumutse ndi kukulanditsa iwe, ati Yehova.


Koma Yehova ali ndi ine ngati wamphamvu ndi woopsa; chifukwa chake ondisautsa adzaphunthwa, sadzandilala; adzakhala ndi manyazi ambiri, chifukwa sanachite chanzeru, ngakhale ndi kunyazitsa kwamuyaya kumene sikudzaiwalika.


Yehova, Mulungu wa Israele atero, Taonani, ndidzabweza zida za nkhondo zimene zili m'manja anu, zimene mumenyana nazo ndi mfumu ya ku Babiloni, ndi Ababiloni akuzinga inu, kunja kwa malinga, ndipo ndidzazisonkhanitsa pakati pa mzinda uwu.


Koma dzanja la Ahikamu mwana wa Safani linali ndi Yeremiya, kuti asampereke m'manja a anthu kuti amuphe.


ndipo iwe sudzapulumuka m'dzanja lake, koma udzagwiridwadi, nudzaperekedwa m'dzanja lake; ndipo maso ako adzaonana nao a mfumu ya ku Babiloni, ndipo iye adzanena nawe pakamwa ndi pakamwa, ndipo udzanka ku Babiloni.


Atero Yehova, Mulungu wa Israele: Muzitero kwa mfumu ya Yuda, imene inakutumani inu kwa Ine kuti mundifunse Ine: Taonani, nkhondo ya Farao, yakutulukira kudzathandiza inu, idzabwerera ku Ejipito ku dziko lao.


koma ngati simudzatulukira kwa akulu a mfumu ya ku Babiloni, mzindawu udzaperekedwa m'dzanja la Ababiloni, ndipo udzatenthedwa ndi moto, ndipo simudzapulumuka m'manja mwao.


Yehova atero, Iye wakukhala m'mzindawu adzafa ndi lupanga, ndi njala, ndi mliri; koma iye wakutulukira kunka kwa Ababiloni adzakhala ndi moyo, ndipo adzakhala nao moyo wake ngati chofunkha, nadzakhala ndi moyo.


Tsopano mudziwetu kuti mudzafa ndi lupanga, ndi njala ndi mliri, komwe mufuna kukakhalako.


Ndakuyesa iwe nsanja ndi linga mwa anthu anga, kuti udziwe ndi kuyesa njira yao.


Anadza naye kwa Yesu. M'mene anamyang'ana iye, anati, Uli Simoni mwana wa Yohane; udzatchedwa Kefa (ndiko kusandulika Petro).


Iye wakupambana, ndidzamyesa iye mzati wa mu Kachisi wa Mulungu wanga, ndipo kutuluka sadzatulukamonso; ndipo ndidzalemba pa iye dzina la Mulungu wanga, ndi dzina la mzinda wa Mulungu wanga, la Yerusalemu watsopano, wotsika mu Mwamba, kuchokera kwa Mulungu wanga; ndi dzina langa latsopano.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa