Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yakobo 2:26 - Buku Lopatulika

26 Pakuti monga thupi lopanda mzimu lili lakufa, koteronso chikhulupiriro chopanda ntchito chili chakufa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

26 Pakuti monga thupi lopanda mzimu lili lakufa, koteronso chikhulupiriro chopanda ntchito chili chakufa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

26 Paja monga momwe thupi lopanda mzimu limakhala lakufa, moteronso chikhulupiriro chopanda ntchito zake nchakufa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

26 Monga thupi lopanda mzimu ndi lakufa, chomwechonso chikhulupiriro chopanda ntchito zabwino ndi chakufa.

Onani mutuwo Koperani




Yakobo 2:26
11 Mawu Ofanana  

Mukabisa nkhope yanu, ziopsedwa; mukalanda mpweya wao, zikufa, ndipo zibwerera kufumbi kwao.


Mpweya wake uchoka, abwerera kunka kunthaka yake; tsiku lomwelo zotsimikiza mtima zake zitayika.


fumbi ndi kubwera pansi pomwe linali kale, mzimu ndi kubwera kwa Mulungu amene anaupereka.


Siyani munthu, amene mpweya wake uli m'mphuno mwake; chifukwa m'mene awerengedwamo ndi muti?


Ndipo pamene Yesu anafuula ndi mau aakulu, anati, Atate, m'manja mwanu ndipereka mzimu wanga. Ndipo pakutero anapereka mzimu wake.


Pakuti mwa Khristu Yesu kapena mdulidwe kapena kusadulidwa kulibe mphamvu; komatu chikhulupiriro, chakuchititsa mwa chikondi.


Chipindulo chake nchiyani, abale anga, munthu akanena, Ndili nacho chikhulupiriro, koma alibe ntchito? Kodi chikhulupirirocho chikhoza kumpulumutsa?


Momwemonso chikhulupiriro, chikapanda kukhala nacho ntchito, chikhala chakufa m'kati mwakemo.


Koma ufuna kuzindikira kodi, munthu wopanda pake iwe, kuti chikhulupiriro chopanda ntchito chili chabe?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa