Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yakobo 2:15 - Buku Lopatulika

15 Mbale kapena mlongo akakhala wausiwa, ndi kusowa chakudya cha tsiku lake,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Mbale kapena mlongo akakhala wausiwa, nichikamsowa chakudya cha tsiku lake,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Mwachitsanzo: mbale wina kapena mlongo ali ndi usiŵa, ndipo masiku onse alibe chakudya chokwanira.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Tangoganizirani, mʼbale kapena mlongo amene ali ndi usiwa, ndipo alibe chakudya cha tsiku ndi tsiku.

Onani mutuwo Koperani




Yakobo 2:15
11 Mawu Ofanana  

ndipo ngati upereka kwa wanjala chimene moyo wako umakhumba, ndi kukhutitsa moyo wovutidwa, pomwepo kuunika kwako kudzauka mumdima, ndipo usiku wako udzanga usana;


Kodi si ndiko kupatsa chakudya chako kwa anjala, ndi kuti ubwere nao kunyumba kwako aumphawi otayika? Pakuona wamaliseche kuti umveke, ndi kuti usadzibisire wekha a chibale chako?


wosasautsa munthu aliyense, koma wambwezera wangongole chigwiriro chake, wosatenga zofunkha, anampatsa wanjala chakudya chake, naveka wamaliseche ndi chovala,


Pakuti muli nao aumphawi pamodzi ndi inu masiku onse, ndipo paliponse pamene mukafuna mukhoza kuwachitira zabwino; koma Ine simuli nane masiku onse.


Koma iye anayankha nanena kwa iwo, Iye amene ali nao malaya awiri apatse kwa iye amene alibe; ndi iye amene ali nazo zakudya achite chomwecho.


ndipotu analankhula natsutsana ndi Agriki; koma anayesayesa kumupha iye.


anaponyedwa miyala, anachekedwa pakati, anayesedwa, anaphedwa ndi lupanga, anayendayenda ovala zikopa zankhosa, ndi zikopa zambuzi, nakhala osowa, osautsidwa, ochitidwa zoipa,


Mverani, abale anga okondedwa; kodi Mulungu sanasankhe osauka a dziko lapansi akhale olemera ndi chikhulupiriro, ndi olowa nyumba a ufumu umene adaulonjeza kwa iwo akumkonda Iye?


Koma iye amene ali nacho chuma cha dziko lapansi, naona mbale wake ali wosowa ndi kutsekereza chifundo chake pommana iye, nanga chikondi cha Mulungu chikhala mwa iye bwanji?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa