Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Tito 1:14 - Buku Lopatulika

14 osasamala nthano zachabe za Chiyuda, ndi malamulo a anthu opatuka kusiyana nacho choonadi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 osasamala nthano zachabe za Chiyuda, ndi malamulo a anthu opatuka kusiyana nacho choonadi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 m'malo momasamala nthano zachiyuda, ndi malamulo a anthu okana choona.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 kuti asasamalenso nthano za Chiyuda, ndi malamulo a anthu amene akukana choonadi.

Onani mutuwo Koperani




Tito 1:14
10 Mawu Ofanana  

Ndipo Ambuye anati, Popeza anthu awa ayandikira ndi Ine ndi m'kamwa mwao, nandilemekeza ndi milomo yao, koma mtima wao uli kutali ndi Ine, ndi mantha ao akundiopa Ine, ndi lamulo la anthu analiphunzira;


Koma andilambira Ine kwachabe, ndi kuphunzitsa maphunzitso, malangizo a anthu.


Koma andilambira Ine kwachabe, ndi kuphunzitsa maphunzitso, malangizo a anthu.


koma tsopano, podziwa Mulungu inu, koma makamaka podziwika ndi Mulungu, mubwereranso bwanji kutsata miyambo yofooka ndi yaumphawi, imene mufuna kubwerezanso kuichitira ukapolo?


(ndizo zonse zakuonongedwa pochita nazo), monga mwa malangizo ndi maphunziro a anthu?


ndipo adzalubza dala pachoonadi, nadzapatukira kutsata nthano zachabe.


podziwa kuti wotereyo wasandulika konse, nachimwa, nakhala wodzitsutsa yekha.


Penyani musakane wolankhulayo. Pakuti ngati iwowa sanapulumuke, pomkana Iye amene anawachenjeza padziko, koposatu sitidzapulumuka ife, odzipatulira kwa Iye wa Kumwamba;


Chidawachitikira iwo monga mwa mwambi woona uja, Galu wabwerera kumasanzi ake, ndi nkhumba idasambayi yabwerera kukunkhulira m'thope.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa